Zamkatimu
April 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
May 30, 2011–June 5, 2011
Tiziona Kuti Kutumikira Yehova Ndi Chinthu Chofunika Kwambiri
TSAMBA 9
June 6-12, 2011
Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu
TSAMBA 13
June 13-19, 2011
“Makhalidwe Amene Mzimu Woyera Umatulutsa” Amalemekeza Mulungu
TSAMBA 18
June 20-26, 2011
Kodi Mukulola Mzimu wa Mulungu Kukutsogolerani?
TSAMBA 23
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 9-13
M’dzikoli anthu ambiri sazindikira zinthu zofunika kwambiri, koma Akhristu sayenera kutero. Mkhristu ayenera kuona kulambira Yehova kukhala nkhani yofunika kwambiri. Nkhaniyi itithandiza kuona zinthu moyenera. Pogwiritsa ntchito Malemba, itithandizanso kudziwa mmene tiyenera kuonera maudindo athu achikhristu.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 13-17
Anthu ambiri amavutika kusankha zochita. Nkhaniyi itithandiza kudziwa chifukwa chake tiyenera kuphunzira kusankha zochita mwanzeru. Itchulanso mfundo zothandiza zimene tingatsatire kuti tizisankha zinthu zimene zimalemekeza Mulungu.
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 18-27
Kodi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa” ndi ati? Kodi tingatani kuti tikhale nawo? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala nawo? Mukhoza kuyankha mafunso amenewa tikakambirana makhalidwe 9 amene mzimu woyera umatulutsa. Nkhanizi zili ndi mfundo zothandiza zimene anthu ambiri angapindule nazo.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Kodi Mumaona Umboni Wakuti Mulungu Akutitsogolera?
6 Khalanibe Oona Mtima M’dziko la Anthu Osaona Mtima
29 Ndapeza Zinthu Zambiri Zabwino