Zamkatimu
May 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
June 27, 2011–July 3, 2011
Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhalabe Maso’
TSAMBA 7
July 4-10, 2011
Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhala Okonzeka’
TSAMBA 11
July 11-17, 2011
Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu Ndi Ndani?
TSAMBA 16
July 18-24, 2011
‘Nzeru za Mulungu N’zozama’ Kwambiri
TSAMBA 21
July 25-31, 2011
Anthu Amene Amakhulupirira Yehova Amakhala Olimba Mtima
TSAMBA 28
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA 1, 2 TSAMBA 7-15
Nkhani yoyamba ikufotokoza udindo umene aliyense m’banja lachikhristu ali nawo kuti akhalebe maso mwauzimu. Nkhani yachiwiri ikufotokoza zinthu zofunika kwambiri kuti banja lonse lipite patsogolo mwauzimu. Zinthu zake ndizo kukhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi, kukhala ndi zolinga zauzimu ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse.
NKHANI YOPHUNZIRA 3 TSAMBA 16-20
Yehova ayenera kukhala wofunika kwambiri pa moyo wa atumiki ake. Nkhaniyi ikufotokoza zimene tingaphunzire kwa mkazi woyamba, Hava, munthu wokhulupirika, Yobu, ndiponso Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wangwiro wa Mulungu.
NKHANI YOPHUNZIRA 4 TSAMBA 21-25
Pa Aroma chaputala 11, mtumwi Paulo ananena za mtengo wa maolivi wophiphiritsa. Kodi mbali zosiyanasiyana za mtengo umenewu zimaimira chiyani? Pamene tikukambirana tanthauzo lake, tiphunzira zambiri zokhudza cholinga cha Yehova ndiponso tigoma ndi kuzama kwa nzeru zake.
NKHANI YOPHUNZIRA 5 TSAMBA 28-32
Nkhaniyi ikufotokoza Masalimo 3 ndi 4 amene Mfumu Davide analemba. Nyimbo zouziridwa ndi Mulungu zimenezi zimasonyeza kuti tikhoza kukhala olimba mtima ngati timapemphera kuti Yehova atithandize ndiponso ngati timamukhulupirira ndi mtima wonse. Izi ndi zimene Davide anachita pamene anakumana ndi mavuto monga kuukiridwa ndi mwana wake Abisalomu.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Kodi Mumasangalala Kuwerenga Mawu a Mulungu?
6 “Woyang’anira Wabwino Ndiponso Mnzathu Wapamtima”
26 Tsatirani Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wabwino Kwambiri