Zamkatimu
November 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
December 26, 2011–January 1, 2012
“Usadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
TSAMBA 6
January 2-8, 2012
Yendani Mogwirizana ndi Mzimu Kuti Mupeze Moyo ndi Mtendere
TSAMBA 10
January 9-15, 2012
Ndife “Osakhalitsa” M’dziko Loipali
TSAMBA 16
January 16-22, 2012
Thandizani Amuna Kukula Mwauzimu
TSAMBA 24
January 23-29, 2012
Thandizani Ena Kuti Ayenerere Maudindo
TSAMBA 28
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 6-10
Kodi mukugwiritsira ntchito bwino mwayi wa pemphero umene Mulungu watipatsa? Phunzirani mmene pemphero lingakuthandizireni mukamakumana ndi mavuto, posankha zinthu zofunika kwambiri, kapena mukamalimbana ndi mayesero.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 10-14
Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma kuti aziika maganizo awo pa zinthu za mzimu n’cholinga choti apeze moyo ndi mtendere. Onani mmene mungapindulire ndi malangizo amene anawapatsa.
NKHANI YOPHUNZIRA 3 TSAMBA 16-20
Nkhaniyi ikusonyeza kuti anthu okhulupirika akale ankakhala monga anthu “osakhalitsa m’dzikolo.” Otsatira oyambirira a Yesu anachitanso chimodzimodzi. Nanga bwanji Akhristu masiku ano? M’nkhaniyi tiona tanthauzo la kukhala monga anthu osakhalitsa m’dziko loipali.
NKHANI ZOPHUNZIRA 4, 5 TSAMBA 24-32
Mu mpingo mukufunika amuna ambiri kuti azitsogolera pa zinthu zauzimu. Yesu anathandiza amuna ambiri kumva uthenga wabwino ndiponso kuyenerera maudindo ena. Tiyeni tione njira zimene iye ankagwiritsa ntchito n’cholinga choti nafenso tithandize anthu amene timakumana nawo mu utumiki. Tionanso mmene tingathandizire amuna obatizidwa kuti ayenerere maudindo m’gulu la Yehova.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera
15 “Panopa Ndine Wolumala, Koma Sindidzakhala Chonchi Mpaka Kalekale”
21 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
22 Kodi Mumasangalala ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”?