Zamkatimu
May 15, 2012
© 2012 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA
JULY 2-8, 2012
Muziyamikira Mphatso ya Ukwati Yochokera kwa Mulungu
TSAMBA 3 • NYIMBO: 87, 75
JULY 9-15, 2012
Musataye Mtima Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino
TSAMBA 8 • NYIMBO: 36, 69
JULY 16-22, 2012
Khulupirirani Yehova, Mulungu wa “Nthawi ndi Nyengo”
TSAMBA 17 • NYIMBO: 116, 135
JULY 23-29, 2012
Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?
TSAMBA 23 • NYIMBO: 93, 89
CHOLINGA CHA NKHANI ZOPHUNZIRA
NKHANI ZOPHUNZIRA 1, 2 TSAMBA 3-12
Nkhanizi zikusonyeza kuti kutsatira malangizo a Yehova pa nkhani ya ukwati n’kofunika kwambiri. Zitithandizanso kuyamikira kwambiri mphatso ya ukwati imene Mulungu wapereka. Zikufotokozanso kuti ngati banja lathu silikuyenda bwino sitiyenera kutaya mtima. Komanso zikufotokoza mmene kutsatira malangizo a m’Malemba kungatithandizire kuti tikhale ndi banja losangalala.
NKHANI YOPHUNZIRA 3 TSAMBA 17-21
Nkhaniyi ikufotokoza kuti Yehova amachita zinthu pa nthawi yake. Itithandiza kukhulupirira kwambiri Mulungu komanso Mawu ake, Baibulo. Itilimbikitsanso kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi yathu pamene tikuyembekezera mosakayikira kuti Yehova atipulumutsa.
NKHANI YOPHUNZIRA 4 TSAMBA 23-27
Anthufe ndife opanda ungwiro koma timakonda Mulungu. Komanso timafunitsitsa kuonetsa ulemerero wa Yehova. Nkhaniyi ikufotokoza mmene tingachitire zimenezi. Ikusonyezanso zimene tiyenera kuchita kuti tizitsanzira Mulungu ndiponso kumusangalatsa. (Aef. 5:1) Ikufotokozanso mmene tingapitirizire kuonetsa ulemerero wake.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
13 Ndinkakonda kucheza ndi Achikulire anzeru
22 Mafunso ochokera kwa Owerenga
28 “Samalani ndi chofufumitsa cha Afarisi”
31 Kale lathu
PATSAMBA LOYAMBA: Banja lomwe likuchita upainiya likulalikira kwa dalaivala pamalo oimika magalimoto akuluakulu mumzinda wa Toulouse ku France. Magalimoto akuluakulu oposa 1,800, ochokera mayiko osiyanasiyana a ku Ulaya, amadutsa mumzindawu tsiku lililonse.
FRANCE
KULI ANTHU OKWANA
63,787,000
KULI OFALITSA OKWANA
122,433
M’ZAKA 5 ZAPITAZI, APAINIYA AWONJEZEKA NDI:
119 Peresenti