Zamkatimu
November 15, 2012
© 2012 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino ndi wathu.
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA
DECEMBER 24-30, 2012
“Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”
TSAMBA 3 • NYIMBO: 69, 120
DECEMBER 31, 2012–JANUARY 6, 2013
Yesu Anatipatsa Chitsanzo cha Kudzichepetsa
TSAMBA 10 • NYIMBO: 84, 82
JANUARY 7-13, 2013
Yesetsani Kukhala Ngati Wamng’ono
TSAMBA 15 • NYIMBO: 26, 68
JANUARY 14-20, 2013
Yehova Ndi Wofunitsitsa Kukukhululukirani
TSAMBA 21 • NYIMBO: 67, 91
JANUARY 21-27, 2013
Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse
TSAMBA 26 • NYIMBO: 77, 118
CHOLINGA CHA NKHANI ZOPHUNZIRA
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 3-7
Mfumu Davide inkalemekeza kwambiri dzina la Yehova ndiponso cholinga chake. Nkhaniyi ikusonyeza kuti Davide ankalemekezanso mfundo za m’Chilamulo cha Mulungu ndipo ankapemphera kuti Mulungu amuphunzitse kuchita chifuniro chake. Nkhaniyi itithandizanso kuona kuti nthawi zonse tiyenera kuyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera.
NKHANI ZOPHUNZIRA 2, 3 TSAMBA 10-19
Akhristu oona amadziwa kufunika kokhala odzichepetsa chifukwa amatsatira chitsanzo cha Yesu. Nkhani yoyamba ikufotokoza chitsanzo cha Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa ndipo itithandiza kuti tiziyesetsa kumutsanzira. Nkhani yachiwiri ikusonyeza zimene tingachite kuti tizikhala ngati wamng’ono.
NKHANI ZOPHUNZIRA 4, 5 TSAMBA 21-30
Nkhani zimenezi zitithandiza kudziwa kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululuka ngakhale machimo akuluakulu. Nthawi zina ifeyo tingavutike kukhululukira ena. Koma mfundo za m’Malemba zingatithandize kukhala ndi mtima wokhululuka.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
8 Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa
20 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
31 Kale Lathu
PATSAMBA LOYAMBA: Akulalikira m’katauni kakumidzi kotchedwa Albarracín kuchigawo chapakati m’dziko la Spain. Mu mpingo wa Teruel muli ofalitsa 78 ndipo m’gawo lake muli katauni ka Albarracín ndi matauni ena okwana 188
SPAIN
KULI ANTHU
47,042,900
KULI OFALITSA
111,101
OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO MU 2012
192,942