Zamkatimu
December 15, 2012
© 2012 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA
JANUARY 28, 2013–FEBRUARY 3, 2013
Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri
TSAMBA 4 • NYIMBO: 115, 45
FEBRUARY 4-10, 2013
TSAMBA 9 • NYIMBO: 62, 125
FEBRUARY 11-17, 2013
Pitirizani Kukhala Monga “Anthu Osakhalitsa M’dzikoli”
TSAMBA 19 • NYIMBO: 107, 40
FEBRUARY 18-24, 2013
“Anthu Osakhalitsa M’dzikoli” Ndi Ogwirizana Polambira Mulungu
TSAMBA 24 • NYIMBO: 124, 121
CHOLINGA CHA NKHANI ZOPHUNZIRA
NKHANI ZOPHUNZIRA 1, 2 TSAMBA 4-13
Kodi moyo wabwino umatanthauza chiyani? Nkhanizi zikusonyeza kuti yankho la funsoli ndi losiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri m’dzikoli angayankhe. Zikusonyezanso kuti tingakhale ndi moyo wabwino tikamakhala okhulupirika kwa Mulungu ndiponso kukwaniritsa maudindo amene watipatsa.
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 19-28
Kodi Akhristu odzozedwa ndiponso anzawo a “nkhosa zina” amakhala bwanji “osakhalitsa m’dzikoli”? (Yoh. 10:16; 1 Pet. 2:11) Nkhanizi zitithandiza kudziwa yankho lake. Zitilimbikitsanso kukhalabe “osakhalitsa m’dzikoli” komanso kugwirizana ndi abale padziko lonse pogwira ntchito yolalikira.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Tisamagwiritse Ntchito Baibulo Ngati Chithumwa
14 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
29 Cholinga cha Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta
32 Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda a 2012
PATSAMBA LOYAMBA: M’dziko la South Korea muli Mboni zoposa 100,000. Mboni zambiri zili m’ndende chifukwa chosalowerera ndale ndiponso kukana usilikali. Ngakhale m’ndendemo, amayesetsabe kulalikira. Ena amalalikira polemba makalata
KU SOUTH KOREA
KULI ANTHU
48,184,000
KULI OFALITSA
100,059
ABALE OMWE ANALI M’NDENDE CHAKA CHATHA
731
MWEZI ULIWONSE, ANKALALIKIRA MAOLA
9,000