Zamkatimu
May 15, 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
JULY 1-7, 2013
Muzigwira Bwino Ntchito Yanu Yolalikira
TSAMBA 3 • NYIMBO: 103, 102
JULY 8-14, 2013
Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?
TSAMBA 8 • NYIMBO: 108, 93
JULY 15-21, 2013
Muzilankhulana Bwino Kuti Banja Lanu Likhale Lolimba
TSAMBA 14 • NYIMBO: 36, 87
JULY 22-28, 2013
Makolo ndi Ana Ayenera Kulankhulana Mwachikondi
TSAMBA 19 • NYIMBO: 88, 3
JULY 29, 2013–AUGUST 4, 2013
Muzisankha Zinthu Mwanzeru Kuti Musataye Madalitso Anu
TSAMBA 26 • NYIMBO: 14, 134
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Muzigwira Bwino Ntchito Yanu Yolalikira
Kodi mlaliki amachita chiyani? Nkhaniyi iyankha funso limeneli ndipo ikusonyeza chifukwa chake anthu akufunikira kumva uthenga wabwino. Ikufotokozanso zimene tingachite kuti tizigwira bwino ntchito yathu yolalikira.
▪ Kodi Ndinu “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?
Nkhaniyi ikufotokoza mmene kukhala “odzipereka pa ntchito zabwino” kungathandizire kuti anthu ayambe kuphunzira za Mulungu. (Tito 2:14) Ikufotokoza mmene khama lathu polalikira ndiponso khalidwe lathu labwino zimathandizira.
▪ Muzilankhulana Bwino Kuti Banja Lanu Likhale Lolimba
▪ Makolo ndi Ana Ayenera Kulankhulana Mwachikondi
Mwamuna ndi mkazi ayenera kulankhulana bwino kuti azisangalala m’banja. Nkhani yoyamba ikufotokoza makhalidwe amene angatithandize kuti tizilankhulana bwino. Nkhani yachiwiri ikusonyeza zimene makolo ndi ana angachite kuti asamavutike kulankhulana bwino.
▪ Muzisankha Zinthu Mwanzeru Kuti Musataye Madalitso Anu
Kodi Akhristu ali ndi madalitso ati? Kodi tingaphunzire zotani zokhudza madalitsowo pa zimene Esau anachita? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kusankha mwanzeru pa nkhani zokhudza madalitso athu? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhaniyi.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
13 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
24 Zimene Zatithandiza Kukhalabe Osangalala
31 Kale Lathu
PATSAMBA LOYAMBA: Alongowa ali ku London ndipo akulalikira kwa mwinisitolo pogwiritsa ntchito kabuku ka m’chinenero cha Chigujarati
LONDON KU ENGLAND