Zamkatimu
October 15, 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
DECEMBER 2-8, 2013
Chilengedwe Chimatithandiza Kukhulupirira Kwambiri Mulungu
TSAMBA 7 • NYIMBO: 110, 15
DECEMBER 9-15, 2013
“Tumikirani Yehova Monga Akapolo”
TSAMBA 12 • NYIMBO: 62, 84
DECEMBER 16-22, 2013
Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Pemphero Limene Linakonzedwa Bwino?
TSAMBA 21 • NYIMBO: 68, 6
DECEMBER 23-29, 2013
Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Yesu
TSAMBA 26 • NYIMBO: 57, 56
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Chilengedwe Chimatithandiza Kukhulupirira Kwambiri Mulungu
Mulungu amene sitingathe kumuona analenga zinthu zonse zimene timatha kuziona. Kodi mumakhulupirira zimenezi ndi mtima wanu wonse? Koma anthu ena sakhulupirira zimenezi. Kodi anthu otero tingawathandize bwanji kudziwa zoona zenizeni zokhudza Mlengi kwinaku tikulimbitsa chikhulupiriro chathu? Nkhani ino itithandiza kuyankha funso limeneli.
▪ “Tumikirani Yehova Monga Akapolo”
Akhristu akulimbikitsidwa kutumikira Yehova monga akapolo. M’nkhaniyi tiona zimene Chilamulo cha Mose chinanena zokhudza akapolo ndiponso zimene tingachite kuti tipewe kukhala akapolo a Satana ndi zinthu zokopa za m’dzikoli. Komanso tiona ubwino wotumikira Mulungu mokhulupirika ngati akapolo.
▪ Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Pemphero Limene Linakonzedwa Bwino?
▪ Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Yesu
Tikamaganizira Mawu a Mulungu mozama tsiku ndi tsiku, mapemphero athu adzakhala ogwira mtima. Umu ndi mmene zinalili pamene Alevi anapemphera m’malo mwa anthu a Mulungu. Nkhani yachiwiri ikusonyeza mmene tingachitire zinthu mogwirizana ndi pemphero lina la Yesu. Mapemphero onsewa akusonyeza ubwino woika patsogolo zofuna za Yehova osati zofuna zathu.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
3 Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Philippines
PATSAMBA LOYAMBA: M’bale akulalikira ku Panajachel, tauni yaing’ono imene ili m’mphepete mwa nyanja ya Atitlan. Kuwonjezera pa Chisipanishi, Mboni za Yehova ku Guatemala zimalalikira uthenga wabwino m’zinenero 11
GUATEMALA
KULI ANTHU OKWANA:
15,169,000
KULI OFALITSA OKWANA:
34,693
MAPHUNZIRO A BAIBULO:
47,606