Zamkatimu
November 15, 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
DECEMBER 30, 2013–JANUARY 5, 2014
“Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphera”
TSAMBA 3 • NYIMBO: 67, 81
JANUARY 6-12, 2014
Pitirizani ‘Kuyembekezera Moleza Mtima’
TSAMBA 10 • NYIMBO: 119, 32
JANUARY 13-19, 2014
Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?
TSAMBA 16 • NYIMBO: 43, 123
JANUARY 20-26, 2014
Muzimvera Abusa Amene Yehova Watipatsa
TSAMBA 21 • NYIMBO: 125, 122
JANUARY 27, 2014–FEBRUARY 2, 2014
Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu
TSAMBA 26 • NYIMBO: 5, 84
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ “Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphera”
Pamene mapeto a dziko loipa la Satanali akuyandikira, tiyenera kuyesetsa kukhala maso mwauzimu. M’nkhani ino tiona kuti kuchita khama popemphera kungatithandize kuchita zimenezi.
▪ Pitirizani ‘Kuyembekezera Moleza Mtima’
M’nkhani ino tiona zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha mneneri Mika pa nkhani ya kuleza mtima. Tionanso zimene zidzasonyeze kuti Yehova watsala pang’ono kuwononga dziko loipali. Komanso tiona zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira kuleza mtima kwa Mulungu.
▪ Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?
Tingaphunzire zambiri pa zimene zinachitika Senakeribu ataukira Yerusalemu m’nthawi ya Hezekiya. Nkhaniyi ingathandize kwambiri akulu amene apatsidwa udindo woweta nkhosa za Mulungu.
▪ Muzimvera Abusa Amene Yehova Watipatsa
▪ Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu
Nkhani yoyamba ikufotokoza mmene Yehova ndi Yesu amawetera nkhosa zawo zapadziko lapansi masiku ano komanso zimene nkhosazo ziyenera kuchita. Nkhani yachiwiri ikufotokoza mtima umene akulu ayenera kusonyeza pamene akuweta nkhosa za Mulungu monga abusa aang’ono.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI
8 Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena?
15 Kutumikira Mulungu Kuli Ngati Mankhwala Ake
31 Kale Lathu
PATSAMBA LOYAMBA: Akulalikira mumsewu pasiteshoni ya sitima ku Tokyo. Anthu oposa 2.8 miliyoni amapita ku Tokyo tsiku lililonse kukagwira ntchito. Choncho abale ndi alongo akuyesetsa kulalikira kwa anthu amene sapezeka pakhomo
JAPAN
KULI ANTHU OKWANA:
126,536,000
KULI OFALITSA OKWANA:
216,692
APAINIYA OKHAZIKIKA:
65,245