Zamkatimu
July 15, 2015
© 2015 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI YOPHUNZIRA
AUGUST 31, 2015–SEPTEMBER 6, 2015
Tizithandiza Kukongoletsa Gulu la Yehova
TSAMBA 7
SEPTEMBER 7-13, 2015
“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”
TSAMBA 14
SEPTEMBER 14-20, 2015
Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Mulungu
TSAMBA 22
SEPTEMBER 21-27, 2015
Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
TSAMBA 27
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Tizithandiza Kukongoletsa Gulu la Yehova
M’gulu la Yehova, Akhristu amakhala pa mtendere ndiponso amagwirizana. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi wokhala m’gululi? Nanga tingathandize bwanji kuti lipitirize kukhala losangalatsa? M’nkhaniyi tipeza mayankho a mafunso amenewa.
▪ “Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”
Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zochititsa chidwi zimene zichitike m’tsogolomu. Ikusonyezanso kuti anthu a Yehova sayenera kuopa chisautso chachikulu.
▪ Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Mulungu
M’dziko la Satanali anthu ambiri amakonda kwambiri dziko lawo, chikhalidwe chawo kapena mtundu wawo. Koma Mkhristu aliyense analonjeza kuti adzakhala wokhulupirika kwa Yehova. Nkhaniyi ikufotokoza chifukwa chake sitilowerera m’mikangano ya m’dzikoli komanso mmene tingadziphunzitsire kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu.
▪ Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
Padziko lonse, anthu a Yehova amasonkhana m’Nyumba za Ufumu kapena malo ena. Nkhaniyi itithandiza kuti tizilemekeza Nyumba za Ufumu, tizizisamalira bwino komanso tizithandiza kuti nyumba zina zimangidwe. Tikatero tidzalemekeza kwambiri Yehova.
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI
3 Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Russia
12 Pitirizani Kutumikira Yehova ‘M’masiku Oipa’
PATSAMBA LOYAMBA: Abale ndi alongo akulalikira kumadera a ku Siberia. Apa tsopano akumana kuti adye chakudya chamasana
RUSSIA
KULI ANTHU
143,930,000
KULI OFALITSA