Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 4 tsamba 8
  • N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Kudziwa Mmene Baibulo Linapulumukira N’kothandiza?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?
    Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 4 tsamba 8
Munthu akuwerenga Baibulo

NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO​—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka?

Masiku ano mukhoza kupeza ndiponso kuwerenga Baibulo mosavuta. Ndipo ngati mwasankha Baibulo lomwe linamasuliridwa molondola, m’posavuta kutsimikizira kuti uthenga wake ndi wochokeradi m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo.a M’nkhani zapitazi taona kuti Baibulo linapulumuka ngakhale kuti likanatha kuwola, anthu ena ankalitsutsa, komanso ankafuna kusintha uthenga wake. Koma n’chifukwa chiyani linapulumuka modabwitsa chonchi?

“Panopa sindikukayika ngakhale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu”

Anthu ambiri amene akuphunzira Baibulo amavomereza zomwe mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Anthuwa amakhulupirira kuti Baibulo linapulumuka chifukwa chakuti ndi Mawu a Mulungu komanso Iye analiteteza. Faizal yemwe watchulidwa m’nkhani yoyambirira, anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo pofuna kutsimikizira zimenezi. Iye anadabwa ataona kuti zinthu zambiri zimene anthu amaphunzitsa m’matchalitchi awo sizichokera m’Baibulo. Faizal anachita chidwi kwambiri ataphunzira cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi kuchokera m’Baibulo.

Iye ananena kuti: “Panopa sindikukayika ngakhale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Komanso ngati Mulungu yemwe ndi Wamphamvuyonse anakwanitsa kulenga chilengedwechi, kodi angalephere kutipatsa buku ndi kuliteteza kuti tiziliwerenga? Munthu yemwe angatsutse zimenezi ndiye kuti akuderera mphamvu za Mulungu, yemwe ndi Wamphamvuyonse, nanga ine ndani kuti ndichite zimenezi?”​—Yesaya 40:8.

a Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008.

Kodi tingatsimikize bwanji kuti Baibulo ndi lolondola?

Nkhanizi zafotokoza zomwe zinathandiza kuti Baibulo lisawonongedwe. Koma n’chiyani chingakutsimikizireni kuti Baibulo ndi “mawu a Mulungu” osati buku la nthano zongolembedwa ndi anthu? (1 Atesalonika 2:13) Tikukulimbikitsani kuti muonere vidiyo ya pa jw.org/ny yakuti, Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? (Pitani pamene palembedwa kuti, MABUKU > MAVIDIYO)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena