Mawu Oyamba
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
Kodi angelo alipodi? Baibulo limati:
“Tamandani Yehova, inu angelo ake amphamvu, ochita zimene wanena, mwa kumvera malamulo ake.”—Salimo 103:20.
Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya angelo komanso mmene angatithandizire.