Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 6 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Aramagedo n’chiyani?
  • Kodi n’zotheka kudzapulumuka pa nkhondo ya Aramagedo?
  • Armagedo—Liti?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Armagedo Ndi Chiyambi cha Moyo Wosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Zimene Anthu Ena Amanena Zokhudza Aramagedo
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 6 tsamba 16
Anthu a “khamu lalikulu” ochokera padziko lonse apulumuka pa Aramagedo

“Khamu lalikulu la anthu” osawerengeka ochokera m’mitundu yonse lidzapulumuka pa Aramagedo

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Aramagedo n’chiyani?

Anthu ena amakhulupirira kuti . . .

ndi nthawi imene dziko lonseli lidzawonongedwe ndi zida za nyukiliya kapena chifukwa cha kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

Aramagedo ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Pa nkhondoyi Mulungu adzawononga anthu onse ochita zoipa.​—Chivumbulutso 16:14, 16.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mulungu adzamenya nkhondo ya Aramagedo osati ndi cholinga chofuna kuwononga dziko lapansili, koma pofuna kuliteteza kuti anthu asapitirize kuliwononga.​—Chivumbulutso 11:18.

  • Nkhondo ya Aramagedo idzathetsa nkhondo zonse.​—Salimo 46:8, 9.

Kodi n’zotheka kudzapulumuka pa nkhondo ya Aramagedo?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Khamu lalikulu la anthu” ochokera m’mitundu yonse lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chomwe chidzathere pa nkhondo ya Aramagedo.​—Chivumbulutso 7:9, 14.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mulungu akufuna kuti anthu ambiri adzapulumuke pa Aramagedo. Iye amachenjeza kaye anthu oipa ndipo amawawononga pokhapokha ngati sanasinthe.​—Ezekieli 18:32.

  • Baibulo limafotokoza zimene tingachite kuti tidzapulumuke pa Aramagedo.​—Zefaniya 2:3.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 8 m’buku ili, Zimene Baibulo Limaphunzitsa, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena