Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA MAY 29, 2017–JUNE 4, 2017
3 “Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”
Kodi inuyo munalonjeza Yehova zinthu zingati? Chimodzi, ziwiri kapena zambiri? Kodi mukuyesetsa kukwaniritsa zimene munalonjezazo? Mwachitsanzo, kodi mukuyesetsa kukwaniritsa zimene munalonjeza podzipereka kwa Mulungu komanso pa tsiku la ukwati wanu? M’nkhaniyi tiona kuti ndi bwino kutsanzira Yefita ndi Hana n’kumakwaniritsa zimene tinalonjeza kwa Yehova.
MLUNGU WA JUNE 5-11, 2017
9 Kodi Ufumu wa Mulungu Ukadzabwera Udzachotsa Zinthu Ziti?
Nthawi zambiri timaganizira zimene Yehova adzatipatse m’Paradaiso. Koma m’nkhaniyi tikambirana zinthu zimene adzachotse. Kodi Mulungu adzachotsa zinthu ziti kuti anthu m’dzikoli adzakhale mwamtendere komanso mosangalala? Kuganizira yankho la funsoli kungalimbitse chikhulupiriro chathu ndiponso kungatithandize kuti tizipirira tikakumana ndi mavuto.
14 Mbiri ya Moyo Wanga—Ndine Msilikali wa Khristu
MLUNGU WA JUNE 12-18, 2017
18 “Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Amachita Zachilungamo
MLUNGU WA JUNE 19-25, 2017
23 Kodi Mumatsanzira Yehova pa Nkhani ya Chilungamo?
Zimakhala zovuta kuti munthu akhalabe wokhulupirika komanso wodzichepetsa akamaganiza kuti anthu ena amuchitira zinthu zopanda chilungamo. M’nkhanizi tikambirana zitsanzo zitatu za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tizitsanzira Yehova pa nkhani ya chilungamo.
MLUNGU WA JUNE 26, 2017–JULY 2, 2017
28 Kudzipereka Kwathu Kumachititsa Kuti Yehova Atamandidwe
Yehova sasowa kalikonse komabe amasangalala ndi zimene timachita tikamayesetsa kuti tikhale kumbali ya ulamuliro wake. Oweruza chaputala 4 ndi 5 akusonyeza kuti Yehova amayamikira tikamayesetsa kutsatira malangizo ake.