Zilengezo
◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu April ndi May: Masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda. June: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. July: Mabrosha a Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene idzafuna zinthu za mkupiti zotchulidwazo iyenera kuziodetsa pa fomu yawo yotsatira ya mwezi ndi mwezi ya Literature Order (S-14).
◼ Kumene kuli kotheka, akulu ayenera kupanga makonzedwe kuti mpingo udzikhala ndi phande m’kuchitira umboni madzulo popeza kuti anthu ambiri amakhala panyumba.
◼ Kwa oyang’anira otsogoza: Tikupemphani kutumiza ku Sosaite zokumana nazo zabwino zilizonse zimene mpingo wanu wakhala nazo mkati mwa chaka, kuphatikizapo zokumana nazo zonena za utumiki waupainiya wothandiza ndi masiku apadera a magazini, pa April 2 ndi May 7, 1994. Tikufuna kusankha chokumana nacho chabwino koposa cha m’munda wathu kaamba ka lipoti lapachaka. Chonde, tumizani zokumana nazo zimenezi pofika kumapeto kwa May 1994. Chonde kumbukirani kutiuza ngati munthu wopereka chokumana nachoyo ali wofalitsa wokhazikika ndipo ali ndi kaimidwe kabwino ndi mpingo, dzina lake, dzina la mpingo umene amaloŵa ndi madeti amene zokumana nazozo zinachitika.
◼ Mabuku Atsopano Omwe Alipo:
Chicheŵa: Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994; Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1994.