Misonkhano Yautumiki ya April
Mlungu Woyambira April 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi Zilengezo zochokera mu Utumiki Wathu Waufumu. Kumbutsani onse ponena za nkhani yapadera imene idzaperekedwa pa April 10, ya mutu wakuti “Chipembedzo Chowona Chikwaniritsa Zofunika za Chitaganya cha Anthu.” Kuyesayesa kwapadera kuyenera kupangidwa kuthandiza atsopano kuti adzafikepo. Ndiponso limbikitsani ofalitsa kuchita upainiya wothandiza m’May.
Mph. 15: “Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini a Chowonadi.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvetsera kufotokoza njira zimene agwiritsira ntchito kuti awonjezere kugaŵira magazini. Itanani ena kudzasimba zokumana nazo ngati nthaŵi ilola.
Mph. 20: “Gaŵirani Magazini Abwino Koposa m’Dziko.” Kambitsiranani nkhaniyo ndi omvetsera, mukumagogomezera mapindu apadera a magaziniwo. Pokambitsirana ndime 2, pemphani wofalitsa wogwira mtima kufotokoza mmene munthu angakhalire wozoloŵerana ndi zamkati ndi mmene angakonzekerere ulaliki. Linganizani zitsanzo ziŵiri zosonyeza njira zogaŵirira makope a April 1 ndi 15. Malizani nkhaniyi mwa kupereka malingaliro ena pankhani zimene zingagwiritsiridwe ntchito pogaŵira masabusikripishoni.
Nyimbo Na. 69 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambitsiranani mfundo zazikulu za mu Mbali ya Mafunso.
Mph. 15: “Msonkhano Wautumiki Umatikonzekeretsa Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizamoni chitsanzo chosonyeza mmene banja limakonzekerera msonkhanowo; gogomezerani kufunika kwa (1) kukonzekera pasadakhale, (2) kumvetsera mosamalitsa, ndi (3) kutengamo mbali.
Mph. 20: “Tumikirani Yehova Popanda Chochenjeneketsa.” Mphatika. Mafunso ndi mayankho. Kambitsiranani ndime 1 mpaka 6.
Nyimbo Na. 90 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 18
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Ŵerengani lipoti la maakaunti ndi kuyamikira zopereka zilizonse kuchokera ku Sosaite. Ndiponso kambitsiranani za nkhani ya m’bokosi yakuti “Osaperekanso Mabuku pa Ngongole!”
Mph. 15: “Bwererani Kumene Munagaŵira Magazini.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Pemphani ndemanga ponena za chifukwa chake pali kufunika kwa kukhala ozoloŵerana bwino kwambiri ndi zamkati mwa magazini ndi mmene tingachitire pogaŵira masabusikripishoni. Ngati nthaŵi ilola, lolani ofalitsa okhoza bwino kusonyeza maulaliki operekeredwa lingaliro.
Mph. 20: “Tumikirani Yehova Popanda Chochenjeneketsa.” Mphatika. Mafunso ndi mayankho. Kambitsiranani ndime 7 mpaka 12.
Nyimbo Na. 51 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 25
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mbiri Yateokratiki. Nkhani yakuti “Ntchito ya Kunyumba ndi Nyumba.”
Mph. 15: Chikhulupiriro. Nkhani yochokera m’buku la Kukambitsirana, masamba 67-70. Kukambitsirana kwa pakati pa mkulu ndi kagulu ka achichepere. Mkuluyo akufotokoza tanthauzo la chikhulupiriro, ndiyeno akufunsa mafunso kaguluko. Kodi nchifukwa ninji ambiri alibe chikhulupiriro? Kodi maziko a chikhulupiriro chathu nchiyani? Kodi ndimotani mmene tingasungire chikhulupiriro chathu kukhala champhamvu? Kodi ndimotani mmene timasonyezera chikhulupiriro chotero? Mkuluyo akumaliza mwa kuyamikira ndi kulimbikitsa kaguluko.
Mph. 20: “Ukhondo Umalemekeza Mulungu.” Mkulu akukambitsirana nkhaniyo ndi omvetsera. Malizani mwa kubwerezanso mwachidule ndemanga za uphungu umene unaperekedwa mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1989, masamba 15-20.
Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.