Zilengezo
◼ Mabuku amene adzagwiritsiridwa ntchito mu September: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. October: Masabusikripishoni a Galamukani! kapena a Nsanja ya Olonda kapena a magazini aŵiri onsewo. November: New World Translation of the Holy Scriptures ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli m’sitoko, gwiritsirani ntchito Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha pa Dziko Lapansi. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapa iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Order (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi. Chonde odetsani magazini owonjezereka ofunika kaamba ka kugaŵira mu October.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena winawake wosankhidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pake monga momwe kungathekere. Lengezani ku mpingo pamene zimenezi zachitidwa.
◼ Ofalitsa amene akulinganiza kudzatumikira monga apainiya othandiza mu October ayenera kupereka mafomu awo mwamsanga. Zimenezi zidzatheketsa akulu kupanga makonzedwe ofunikira a mabuku ndi magawo.
◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pa masamba 21-3 a mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za anthu alionse ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene angafune kubwezeretsedwa.
◼ Aliyense amene akuyanjana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikripishoni onse atsopano ndi kulembetsanso kwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikripishoni a iwo eni, kupyolera mu mpingo.
◼ Sosaite simatumiza maoda a mabuku a wofalitsa aliyense payekha. Awo amene akufuna kanthu kena angadziŵitse mtumiki wa mabuku, amene adzaphatikiza odayo nthaŵi yomweyo pa oda ya mpingo ya pamwezi ya mabuku. Woyang’anira wotsogoza ayenera kulinganiza chilengezo mwezi uliwonse oda ya mpingo ya pamwezi ya mabuku isanatumizidwe ku Sosaite kotero kuti onse amene akufuna kupeza mabuku adziŵitse mbale wosamalira mabuku.
◼ Monga momwe kunalengezedwera mu Utumiki Wathu Waufumu wa June 1994, October 29, 1994, adzakhala Tsiku lapadera la Magazini. Oyang’anira utumiki akukumbutsidwa kupanga makonzedwe abwino a utumiki wakumunda a tsiku limenelo.
◼ Kuyambira mlungu wa January 2, 1995, buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe lidzaphunziridwa pa malo apakati a Phunziro Labuku Lampingo. Mipingo ikulimbikitsidwa kutumiza maoda awo a mabuku mofulumira.
◼ Zofalitsidwa Zimene Zilipo:
Chingelezi: Watch Tower Publications Index 1991-92, mabaundi voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 1993.