Misonkhano Yautumiki ya September
Mlungu Woyambira September 5
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zoyenerera za mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambitsiranani “Mbali ya Mafunso” mukumagogomezera mmene malipoti a phunziro la Baibulo angathandizire wochititsa phunziro labuku kuthandiza awo a m’kagulu kake.
Mph. 20: “Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu.” Woyang’anira utumiki ndi mkulu wina akambitsirana mfundo zazikulu za m’nkhaniyo. Pendani ntchito ya mpingo ya chaka chapita, mukumayamikira limodzinso ndi kupereka malingaliro a kuwongolera. Gogomezerani chonulirapo cha kuwonjezera phande lathu mu utumiki.
Mph. 15: “Kulitsani Chikondwerero m’Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.” Ofalitsa atatu kapena anayi, kuphatikizapo wachichepere, akambitsirana nkhaniyo choyamba ndiyeno nkuyeseza. Akusonyeza maulaliki aŵiri kapena atatu ndiyeno awapenda, akumapatsana malingaliro othandiza ndi kuyamikirana.
Nyimbo Na. 32 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 12
Mph. 7: Zilengezo za pamalopo.
Mph. 20: “Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho yokambidwa ndi mkulu woyenerera, akumafola ndime kuchokera poyambira nkhaniyo mu mphatika kufikira pa mutu waung’ono wakuti “Thandizo Lofunika m’Nthaŵi ya Kusoŵa.” Gogomezerani kufunika kwa kusayembekezera kufikira kanthu kena katachitika ndi kuyamba kuganiza zochita. Linganizani pasadakhale monga banja tsopano lino—khalani okonzekera!
Mph. 18: “Sanaleke Kuchitira Umboni.” Mafunso ndi mayankho. Sonyezani kuti ngakhale kuti tonsefe sitingathe kuthera nthaŵi yofanana mu utumiki, tiyenera kusangalala ndi kuyesayesa kukhala amtima wonse.
Nyimbo Na. 60 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 19
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Ŵerengani lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro zilizonse za zopereka.
Mph. 15: “Pitirizanibe Kuchita Zochuluka m’Ntchito ya Ambuye.” Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime zofunika.
Mph. 20: “Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo ndi Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Linganizani zitsanzo ziŵiri zogwiritsira ntchito maulaliki olingaliridwawo.
Nyimbo Na. 67 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 26
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Pemphani omvetsera ena kusimba mwachidule zokumana nazo ponena za kugaŵira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha kapena kuyambitsa nalo maphunziro.
Mph. 15: “Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?” Mlankhuli waluso apereka nkhani yomveka bwino kuyambira pa mutu waung’ono wakuti “Thandizo Lofunika m’Nthaŵi ya Kusoŵa” kufikira kumapeto kwa nkhani ya mphatikayo, akumagogomezera phindu la kuchitira zinthu pamodzi ndi akulu ndi Makomiti Olankhulana ndi Zipatala pochita ndi vuto lowopsa la kuchipatala.
Mph. 20: Kugaŵira masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! kapena magazini aŵiri onsewo mu October. Gogomezerani kufunika kwa kugaŵira masabusikripishoni mosasamala kanthu za kukwera mtengo kwa zinthu. Anthu ambiri amayamikira kukhala ndi sabusikripishoni yawoyawo. Mwachitsanzo, wolembetsa wina ku Zambia analembera Sosaite kuti: “Ndili ndi zaka 37. Ndakhala m’choonadi kwa zaka 20. Ndili wachimwemwe kukhala ndi sabusikripishoni yachiŵiri yochokera ku ofesi yatsopano ku Lusakako ku Makeni. Chiyambire 1985 pamene ndinayamba kulembetsa, kufikira chaka chino, ndikusangalala kukhala ndi makope 24 a ine mwini chaka chilichonse. (Chiv. 22:2) Sindidzanyalanyaza kulembetsanso sabusikripishoni yanga mosasamala kanthu kuti mtengo wake ungakwere motani chifukwa cha kuchepa mphamvu kwa kwacha yathu. Yehova adalitsetu ntchito yake.” Ndithudi chiyamikiro chotero kaamba ka magazini abwino koposa chimatisonkhezera kuchirikiza ubwino wa sabusikripishoni m’munda. Gogomezerani kufunika kwa kukonzekera bwino tisananyamuke. Khalani ndi ofalitsa atatu, mmodzi wa iwo akhale wachichepere, asonyeze maulaliki a sabusikripishoni aafupi.
Nyimbo Na. 76 ndi pemphero lomaliza.