Nyimbo 36
“Achimwemwe Ali Ofatsa”
(Mateyu 5:5, NW)
1. M’lungu adalitsa ofatsa;
Chimwemwe nchachikuludi.
Ngakhale amasautsidwa;
Modekha alinda M’lungu.
Sada nkhawa ndi oipa,
Odzitukumula onse.
Amadziŵa kuti iwowa,
Adzafa ngati maudzu.
2. “Kuyambira ubwana wanga,
Tsopano ine ndakula.
Sindinawone wolungama
Akumapempha chakudya.”
Yendani mowongokabe
Khulupilirani M’lungu.
Mukakondwera mwa Yehova,
Ntchito yanu idzadala.
3. Oipa adzatha padziko;
Sadzawonanso pokhala,
Ofatsa adzasangalala
Ndi mtendere wochuluka.
Kufikira kunthaŵiyo
Tisunge Mawu a M’lungu,
Tikumasonyeza chifatso
Muzochita zathu zonse.