Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo ndi Buku la Kukhala Ndi Moyo Kosatha
1 Kukonda anthu kuyenera kutisonkhezera kukhala ofulumira m’kubwerera kukathandiza awo amene amamva njala ndi ludzu la choonadi. (Mat. 5:6) Tiyenera kuzindikira umboni uliwonse wa chikondwerero chimene tingapeze ndi kuchikulitsa ngati tisakufuna kuti chizirale. Kukonzekera ndiko mfungulo ya chipambano.
2 Chonulirapo chathu chiyenera kukhala kuyambitsa maphunziro a Baibulo. (Mat. 28:20) Makope oyambirira kusindikizidwa a buku lakuti Kukhala ndi Moyo Kosatha anaphatikizamo mawu oyamba aŵa: “Limeneli ndi buku labwino koposa kuligwiritsira ntchito pophunzira ndi aliyense, wachichepere kapena wachikulire, mosasamala kanthu za pamene anafika m’maphunziro awo.” Lalembedwa m’njira imene imapangitsa maphunziro kukhala osavuta kuchititsa, likumakhozetsa ngakhale ofalitsa achatsopano kukhala ndi phande. Chipambano chathu m’kuyambitsa maphunziro atsopano chimadalira pa kugwira mtima kwathu m’kupanga maulendo obwereza.
3 Kodi Ndimotani Mmene Tingayambitsire Maphunziro? Pamene tibwerera, kaŵirikaŵiri ndi bwino kugwirizanitsa makambitsirano athu ndi mfundo ina kapena funso linalake lofunsidwa paulendo wathu woyamba. Mwinamwake munakambitsirana za mkhalidwe wa akufa, mukumasiya funso lakuti, “Kodi pali chiyembekezo chotani kwa akufa athu okondedwa?” Fotokozani kuti chiukiriro sichili chiyembekezo chopanda maziko; Baibulo limasimba za zitsanzo zambiri za ziukiriro zimene zachitika kale. Pendani zithunzithunzi za patsamba 167-9. Ndiyeno kambitsiranani zimene zanenedwa m’ndime 1 ndi 2 patsamba 166. Pemphani kudzabweranso kaamba ka kukambitsirana kowonjezereka.
4 Mungakhale mutalankhula kwa kholo limene linasonyeza nkhaŵa ponena za mavuto owonjezereka opezedwa m’kulera ana. Munganene motere m’mawu anu:
◼ “Makolo onse amafunira ana awo zabwino koposa. Baibulo lili ndi malangizo amene angathe kuthandiza makolo kuphunzitsa ana awo kupeza moyo wokhutiritsa umene uli ndi tanthauzo ndi chifuno. Chotero, tikuchirikiza mwamphamvu kuti mabanja aziphunzira Baibulo pamodzi. [Tembenukirani pa ndime 23 patsamba 246.] Chidziŵitso chake chopezedwa chingadzetse madalitso osatha ku banja lonse.” Ŵerengani Yohane 17:3. Sonyezani kufunitsitsa kwanu kubwerera kudzasonyeza banjalo mmene lingayambire phunziro lawo.
5 Ngati muli wofalitsa wachichepere kapena wachatsopano ndipo munalankhula pang’ono za chiyembekezo cha Paradaiso pa kufika kwanu koyamba, bukulo litatsegulidwa patsamba 3, ingonenani motere:
◼ “Baibulo limalonjeza kuti awo amene amachita chifuniro cha Mulungu angathe kuyembekezera kudzakhala ndi moyo m’dziko longa ili, mmene mudzakhala chimwemwe ndi mtendere. Buku ili limasonyeza zimene tiyenera kuchita kuti tilandire dalitso limenelo.” Fotokozani mwachidule njira yathu yophunzirira, ndi kupempha kuti muwasonyeze.
6 Monga ophunzira a Yesu, ife tili ndi thayo la kuthandiza anthu. (Aroma 10:14) Ngati tinagaŵira buku kapena tinakhalapo ndi makambitsirano ena abwino, tili ndi thayo la kukulitsa chikondwererocho. (Mat. 9:37, 38) Ngati tikwaniritsa gawo limeneli moyenera, onse angagaŵane m’madalitso amene amakhalapo.—1 Tim. 4:16.