Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/95 tsamba 8
  • Tsatirani Okondwerera Onse kuti Mupindulitse Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsatirani Okondwerera Onse kuti Mupindulitse Ena
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Thandizani Ena Kuti Apindule
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kukulitsa Chikondwerero pa Maulendo Obwereza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 9/95 tsamba 8

Tsatirani Okondwerera Onse kuti Mupindulitse Ena

1 Kodi chinthu chachikulu chimene chimatithandiza kudziŵa ngati tiyenera kugaŵira wina buku nchiyani? Chidwi chake! Ndi mmenenso zimakhalira pa maulendo obwereza. Nthaŵi iliyonse imene wina achita chidwi pang’ono ndi uthenga wa Ufumu, tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti munthuyo apindule. Chotero timapanga maulendo obwereza ndi cholinga cha kukulitsa chidwi cha munthuyo ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba. Chimenechi ndicho cholinga chathu ngakhale pamene sitinagaŵire buku. Kodi tingachite motani zimenezi?

2 Ngati papitapo munakambitsirana za kuchuluka kwa zothetsa nzeru m’maukwati ndipo munagaŵira buku la “Kukhala ndi Moyo Kosatha”, mungayambe kukambitsirana kwanu motere:

◼ “Ulendo watha, tinakambitsirana za ukwati ndi uphungu wa Baibulo wogwira ntchito umene ungatithandize kupeza chimwemwe chokulirapo. Kodi si zoona kuti zothetsa nzeru zimabuka ngakhale m’mabanja abwino nthaŵi ndi nthaŵi? [Yembekezani yankho.] Baibulo limatipatsa uphungu wabwino koposa umene ungatithandize kuthetsa zovuta m’mabanja. Banja lingadale mwa kuphunzira Baibulo pamodzi.” Tsegulani patsamba 246, ndi kukambitsirana ndime 23. Ŵerengani Yohane 17:3, ndipo pemphani kuthandiza banjalo kuyamba kuphunzira Baibulo panyumbapo.

3 Ngati munalankhula za ana ndi kufunika kwawo kwa kuphunzira, mungapitirize makambitsiranowo motere:

◼ “Tsiku lija tinakambitsirana za maphunziro auzimu amene ana amafuna ndiponso mmene makolo angawathandizire. Makolo ochuluka omwe ndalankhula nawo akuda nkhaŵa ndi khalidwe loipa la achichepere ambiri lerolino. Kodi muganiza bwanji za . . . ? [Tchulani khalidwe lopulupudza la achinyamata lofala m’dera lanu. Yembekezani yankho.] Lekani ndikusonyezeni uphungu wina wothandiza woperekedwa m’Baibulo.” Onani ndime 22 patsamba 246 m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, kambitsiranani mfundo yaikulu, ndi kuŵerenga Aefeso 6:4. Sonyezani kuti kwenikweni ana ochuluka amafuna chilango ndi chitsogozo. Pamene makolo achita khama popereka zimenezo, ana amakhala achimwemwe kwambiri ndiponso khalidwe lawo limakhala lolemekezeka kwambiri. Fotokozani mmene timaphunzirira Baibulo ndi ana athu.

4 Ngati munakambitsirana za dziko lapansi la Paradaiso, mwina munganene zotsatirazi kuti mudzutsenso chidwi:

◼ “Tinaona zithunzithunzi zina m’bukuli zimene zinatisonyeza mmene dziko lapansi lidzakhalira pamene Mulungu adzalipanga kukhala paradaiso. Lingakhale lopanda tanthauzo kwenikweni ngati sitingakhalemo ndi okondedwa athu. Kodi sichoncho?” Yembekezani yankho. Ndiyeno tsegulani patsamba 162 m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4, ndi kufotokoza mmene tingakhalire ndi okondedwa athu nthaŵi zonse. Ngati munthuyo akufunitsitsa, ŵerengani Yohane 5:28, 29 kusonyeza kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. Sonyezani chikuto cha bukulo ndi kunena kuti: “Nzoona—tingakhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi!” Konzani ulendo wina wodzakambitsirana mmene timadziŵira kuti paradaiso ali pafupi.

5 Chifuno chachikulu cha ulendo wobwereza ndicho kuthandiza anthu okondwerera kupindula ndi uthenga wa Ufumu. Anthu ochuluka amafuna kanthu kena kodzutsa njala yawo ya zinthu zauzimu. Asonyezeni mfundo zakutizakuti zothandiza m’bukulo, mukumagogomezera mmene lingawathandizire kumvetsa Baibulo. Maulendo obwereza amene amakwaniritsa zolinga zimenezi adzathandiza ena kupindula kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena