Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero
1 Pamene anatsogozedwa ndi mngelo wa Yehova kwa Mwaitiopiya amene anasonyeza chikondwerero choona m’Mawu a Mulungu a choonadi, wophunzira Filipo mwachikondi anamthandiza kumvetsetsa zimene anali kuŵerenga. (Mac. 8:26-39) Kodi timadzipereka kuti tithandize awo amene akusonyeza chikondwerero? Tiyenera kutero, popeza kuti ntchito yathu yaumulungu imaphatikizapo kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Kodi tingachitenji kuti tiwathandize?
2 Patulani nthaŵi mlungu uliwonse ya maulendo obwereza. Linganizani kufikira awo amene anasonyeza chikondwerero, ndi kuyesa kupitiriza makambitsirano a Malemba amene anayambidwa pa ulendo wanu woyamba. Kumbukirani chonulirapo cha kuyambitsa phunziro la Baibulo. Bwereraniko nthaŵi zonse kuti mukagaŵire makope atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Gaŵirani masabusikripishoni.
3 Ngati munakambitsirana za phindu la Baibulo pa ulendo wanu woyamba, mungapitirize makambitsiranowo, mukumagwiritsira ntchito malingaliro a patsamba 60 la buku la “Kukambitsirana” ndi kunena zonga zotsatirazi:
◼ “Ena amalingalira kuti uphungu wa Baibulo sumagwira ntchito m’dziko lathu lamakono. Kodi muganiza motani pa zimenezo? [Yembekezerani yankho.] Kodi simungavomereze kuti buku lopereka uphungu wanzeru umene ungatikhozetse kukhala ndi moyo wa banja wachimwemwe nlothandiza? [Yembekezerani ndemanga.] Ziphunzitso ndi machitachita zokhudza moyo wa banja zasintha, ndipo zotulukapo zake zimene timaona lerolino sizili zabwino. Koma mabanja amene amagwiritsira ntchito zimene Baibulo limanena ngolimba ndi achimwemwe.” Ŵerengani Akolose 3:18-21. Gaŵirani trakiti lakuti Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo, ndipo longosolani kuti timapereka programu yaulere ya phunziro la Baibulo.
4 Mungayambe makambitsirano onena za mkhalidwe wa akufa motere:
◼ “Pakhala zokambakamba zambiri ponena za mkhalidwe wa akufa. Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chimatichitikira pamene tifa? [Yembekezerani yankho.] Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti timapitirizabe kukhalapo mu mpangidwe wina. Ambiri adabwa pamene adziŵa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. [Ŵerengani Mlaliki 9:5.] Pamene kuli kwakuti akufa sadziŵa kanthu, iwo sanaiŵalike. Mulungu walonjeza kuwaukitsira ku moyo pansi pa ulamuliro wa Ufumu wake.” Tembenukirani ku Nsanja ya Olonda ya October 15, 1994, kapena patsamba 162 la buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, ndi kukambitsirana malemba ndi zithunzi. Linganizani ulendo wina wobwereza, ndi cholinga cha kugaŵira masabusikripishoni ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo.
5 Ngati mukufuna kupereka malongosoledwe owonjezereka onena za lingaliro Lachikristu la nkhondo pakati pa mitundu, munganene motere:
◼ “Ena amakhulupirira kuti kumenyana ndiko njira yokha yothetsera mikangano. Kodi muganiza bwanji ponena za zimenezo? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu akhale pamodzi mu mtendere. [Ŵerengani Aroma 12:17, 18.] Zimenezo zidzachitikadi padziko lonse pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.” Tembenukirani ku brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, pamasamba 25-6. Pemphani kudzabweranso kuti mudzalongosole chifukwa chake Yesu anatiphunzitsa kupempherera ‘chifuniro cha Mulungu kuchitidwa, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’—Mat. 6:10.
6 Mdindo wa ku Aitiopiya anavomereza kusakhoza kwake kumvetsetsa popanda wina womtsogolera. (Mac. 8:31) Mwachikondi Filipo anampatsa thandizo limene anafuna. Ife tingasonyeze chikondi chathu chenicheni kwa ena mwa kuwathandiza mwanjira yofananayo.