Kugwiritsira Ntchito Brosha Latsopano Mogwira Mtima
1 Pa msonkhano wathu wachigawo waposachedwapa, tinasangalala kwambiri kulandira brosha latsopano lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Liyenera kukopa anthu a m’mikhalidwe yonse ya moyo, popeza kuti ambiri akhala ndi chisoni chachikulu pa kutayikiridwa ndi wokondedwa wawo. Zithunzi zake zokopazo ziyenera kupangitsa broshalo kukhala losavuta kugaŵira. Patsamba 29 chithunzi chochititsa chidwi cha Lazaro akuukitsidwa kwa akufa chimasonyeza “chikhumbo . . . chachikulu cha kubwezeretsa awo otengedwa ndi imfa” cha Yesu. Chithunzi cha patsamba lotsatira chimasonyeza mkhalidwe wosangalatsa wa chiukiriro m’dziko latsopano. Zimenezi ziyenera kusonkhezera chotani nanga mitima ya awo ogwidwa ndi chisoni!
2 Brosha limeneli lingakhale lothandiza kwambiri potonthoza ofedwa. Lalembedwa mumpangidwe wokhoza kukambitsirana. Mafunso osonyezera mfundo zazikulu ali m’bokosi pamapeto a chigawo chilichonse mmalo mwa kuikidwa pansi patsamba lililonse. Mungagwiritsire ntchito “Mafunso Owasinkhasinkha” m’njira iliyonse imene mukuganiza kuti idzakhala yothandiza koposa kwa wophunzira wanu.
3 Pofikira anthu, sankhani mfundo zokambitsirana zimene zikupezeka m’broshalo. Inu mungalingalire kuti kungakhale koyenera kusonyeza zamkati patsamba 2 ndi kufunsa mwininyumba kusonyeza nkhani imene ikumkhudza mtima. Zindikirani zosoŵa za munthu aliyense. Mloleni kuti afotokoze malingaliro ake, ndiyeno sonyezani mmene broshalo limaperekera chitonthozo. Chigawo chilichonse chimagwiritsira ntchito malemba a Baibulo okwanira amene amapereka maziko a chiyembekezo chathu.
4 Mutu waung’ono patsamba 5 wakuti, “Pali Chiyembekezo Chenicheni,” umafotokoza za chiyembekezo chotonthoza cha akufa chozikidwa pa Baibulo. Zimenezi ziyenera kusonkhezera chikhumbo cha kukambitsirana za “Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa,” chopezeka pamasamba 26-31. Bokosi la patsamba 27 limapereka “Malemba Amene Amatonthoza” owonjezereka. Mwininyumba wogwidwa ndi chisoni adzaona mwamsanga kuti Yehova alidi “Mulungu wa chitonthozo chonse.”—2 Akor. 1:3-7.
5 M’njira yokhudza mtima, zigawo zamkatimo zimafotokoza za michitidwe yosiyanasiyana pa imfa ya wokondedwa. Zimasonyeza mmene munthu angalimbanire ndi chisoni ndi mmene ena angathandizire panthaŵi yosautsa yotero. Patsamba 25 pali bokosi la mutu wakuti “Kuthandiza Ana Kuchita ndi Imfa.” Umenewu uyenera kukhala wothandiza kwenikweni kwa makolo amene ayenera kulimbana ndi vuto limeneli.
6 Khalani ndi kope lapadera pafupi, ndipo ligwiritsireni ntchito mu umboni wamwamwaŵi. Inu mungafune kukafika kunyumba zamaliro za kwanuko m’gawo lanu kuti mukaone ngati angafune kukhala ndi makope otonthozera mabanja ofedwa. Kapena mwinamwake mwaluso mungafikire anthu ogwidwa ndi chisoni kumanda panthaŵi zimene amakazonda manda a wokondedwa.
7 Tikukondwera kuti Yehova ndiye Mulungu “amene atonthoza odzichepetsa.” (2 Akor. 7:6) Ndi mwaŵi wathu kukhala ndi phande ‘m’kutonthoza amene akulira maliro.’—Yes. 61:2.