Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/08 tsamba 8
  • Limbikitsani Oferedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Limbikitsani Oferedwa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Chitonthozo Chochokera kwa “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kugwiritsira Ntchito Brosha Latsopano Mogwira Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • “Lirani ndi Anthu Amene Akulira”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 4/08 tsamba 8

Limbikitsani Oferedwa

1. N’chifukwa chiyani oferedwa amafunika kulimbikitsidwa?

1 Zimakhala zopweteka munthu amene tinali kum’konda akamwalira, ndipo n’zopweteka kwambiri makamaka kwa anthu amene alibe chiyembekezo cha Ufumu. (1 Ates. 4:13) Kawirikawiri, anthu ambiri amafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani anthu amafa? Kodi anthuwo akafa amapita kuti? Kodi zidzatheka kuonananso ndi munthu amene ndinali kumukonda?’ M’ndime zotsatirazi muli njira zina zolimbikitsira anthu amene timakumana nawo muutumiki wakumunda ndipo ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya m’bale wawo kapena mnzawo.—Yes. 61:2.

2. Ngati mwininyumba watiuza kuti adakali ndi chisoni, kodi tiziyesetsabe kumulalikira nthawi yaitali?

2 Polalikira Nyumba ndi Nyumba: Tiyerekeze kuti mwininyumba watiuza kuti m’bale wake wamwalira posachedwapa. Ndi bwino kudzifunsa mafunso ngati awa: Kodi munthuyo akuoneka kuti adakali ndi chisoni chachikulu? Kodi pakhomopo padzadza achibale amenenso akuoneka kuti ali ndi chisoni? Ngati zili choncho, si bwino kumulalikira nthawi yaitali. (Mlal. 3:1, 7) Mwina tingam’pepese, kum’gawira kapepala, magazini, kapena kabuku koyenerera, kenako n’kutsanzika. Ndiyeno tingadzapitenso nthawi ina yabwino kuti tikapitirize kumulimbikitsa pogwiritsira ntchito Baibulo.

3. Ngati n’kotheka, kodi ndi malemba ati amene tingawerengere mwininyumba yemwe ali pa chisoni?

3 Nthawi zina tingaone kuti n’zotheka kulankhula zambiri paulendo woyamba. Ngakhale kuti imeneyi si nthawi yabwino yotsutsa maganizo olakwika, mwina tingathe kuwerenga nawo malonjezo a m’Baibulo onena za kuuka kwa akufa. (Yoh. 5:28, 29) Kapena tingagwiritse ntchito Baibulo n’kuwafotokozera zimene zimachitika munthu akafa. (Mlal. 9:5, 10) Munthu angalimbikitsidwenso ndi nkhani ya m’Baibulo ya munthu wina amene anaukitsidwa. (Yoh. 11:39-44) Njira ina ingakhale kuwerenga mawu amene Yobu anafotokozamo chiyembekezo chake mwa Yehova. (Yobu 14:14, 15) Tisanachoke pakhomopo tingathe kuwapatsa kabuku kakuti What Happens to Us When We Die?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kapena kabuku kena kalikonse koyenerera, kapenanso kapepala. Mwinanso tingawapatse buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi kuwasonyeza zimene zili m’mutu 6, n’kugwirizana kuti tidzakambirane nawo bwino nkhaniyo.

4. Kodi tingalimbikitse oferedwa pazochitika zina ziti?

4 Pazochitika Zina: Ngati mwambo wa maliro uchitikire m’Nyumba ya Ufumu, kodi padzakhala anthu amene si Mboni? Chifukwa cha anthu amenewa, mwina tingakonze zoti pakhale mabuku amene amalimbikitsa anthu oferedwa. Ogwira ntchito panyumba zina zochitirako mwambo wa maliro amayamikira kukhala ndi mabuku athu kuti azipatsa mabanja oferedwa. Nthawi zina ena akhala ndi mwayi wolembera banja loferedwa kalata yachidule yowalimbikitsa pambuyo poona mauthenga achisoni m’nyuzipepala. Bambo wina yemwe mkazi wake anamwalira, analandira kalata imene inali ndi timapepala ndipo anapita ndi mwana wake wamkazi kunyumba kwa mlongo amene analemba kalatayo ndi kumufunsa kuti: “Kodi ndinu amene munanditumizira kalata iyi? Ndikufuna ndidziwe zambiri za Baibulo.” Bambo ndi mwana wakeyo anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kupita ku misonkhano.

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala tcheru ndi mipata yolimbikitsira anthu amene aferedwa?

5 Lemba la Mlaliki 7:2 limati: “Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero.” N’zosavuta kuti munthu amene ali pa chisoni amvetsere Mawu a Mulungu kusiyana ndi munthu amene ali pa chisangalalo. Tonsefe tiyenera kukhala tcheru ndi mipata imene tingalimbikitsire anthu amene ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya wokondedwa wawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena