Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/97 tsamba 8
  • Thandizani Ena Kupeza Chitonthozo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ena Kupeza Chitonthozo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 7/97 tsamba 8

Thandizani Ena Kupeza Chitonthozo

1 Anthu ambiri atopa ndi kumva za masoka, nkhondo, upandu, ndi kuvutika. Chitonthozo ndi chinthu chimene mtundu wa munthu ukufunadi, ngakhale nzoonekeratu kuti mulibe m’malipoti a panyuzi a masiku ano. Kutonthoza kumatanthauza “kupatsa nyonga ndi chiyembekezo kwa” ndi “kuchepetsa chisoni kapena vuto la” wina. Monga Mboni za Yehova, tili okonzeka kuthandiza anthu pazimenezi. (2 Akor. 1:3, 4) Mabrosha athu ozikidwa pa Baibulo amene tidzagaŵira m’July ndi August ali ndi mauthenga otonthoza a choonadi. (Aroma 15:4) Nazi njira zina zowagaŵira m’mikhalidwe yosiyanasiyana:

2 Nkhani ya panyuzi ya tsoka linalake ingapange mpata wochitira umboni ndi kutonthoza ena, mwinamwake mutanena zonga izi:

◼ “Zinthu zimenezi zikachitika, ena amadabwa ngati Mulungu alikodi ndi kuti, ngati aliko, kaya amasamala za ife. Kodi mukuganizapo bwanji? [Yembekezani yankho.] Njira ina yodziŵira ngati kuli Mulungu ndiyo kugwiritsira ntchito pulinsipulo lotsimikizika.” Ŵerengani Ahebri 3:4. Tchulani zinthu zina zotizinga zimene ndithudi zinachita kupangidwa. Ndiyeno pitirizani kuti: “Ndili ndi brosha limene ndikudziŵa kuti mudzalipeza kukhala lotonthoza. Lili ndi mutu wakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? [Ŵerengani mafunso a pachikuto.] Lili ndi umboni wokhutiritsa wakuti Mulungu sikuti aliko chabe komanso posachedwapa adzathetsa mikhalidwe yonse yosalungama imene tikuyang’anizana nayo lerolino. Kodi mungakonde kuliŵerenga? Lingakhale lanu pachopereka cha K3.60.” Linganizani kubwererako.

3 Paulendo wobwereza, munganene kuti:

◼ “Pamene ndinasiya brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? tinalankhula za umboni wakuti Mulungu aliko. Mwinamwake munaiona mfundoyi patsamba 7. [Sonyezani chithunzicho ndi kufotokoza mwachidule ndime 15.] Ichi nchitsanzo chimodzi chabe chosonyeza kuti Mulungu wosamala alikodi. [Ŵerengani ndime 27 patsamba 9.] Phunziro laumwini la Baibulo landithandiza kupirira mavuto a tsiku ndi tsiku a moyo chifukwa limapereka lingaliro la Mulungu pa nkhanizi.” Pemphani kusonyeza phunzirolo.

4 Mungachite umboni wapafoni mwa kugwiritsira ntchito brosha lakuti “Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?” Mungadzidziŵikitse ndi kunena kuti:

◼ “Ndikuimbirani foni kuti ndikuuzeni uthenga wofunika poti sindingathe kudzakomana nanu.” Ŵerengani ndime yoyamba patsamba 4 la broshalo, ndipo chitani zimenezo mwachibadwa, monga kuti mukumuona munthu amene mukulankhula nayeyo. Mfunseni munthuyo zimene akuganiza, ndipo yembekezani yankho. “Ndatsegula Baibulo langa pa Yesaya 45:18. Vesili likusonyeza kuti dziko lapansi analipangira ife. Kodi ndingakuŵerengereni?” Kenako, fotokozani chifuno cha broshalo, ndipo funsani kuti mungamperekere motani kope lake.

5 Paulendo wachiŵiri, mungayese mafikidwe awa oyambitsira phunziro:

◼ “Ndikufuna kuwonjezera pa zimene tinakambitsirana poyamba mwa kupereka chitsanzo ponena za amene angatiuze chifuno cha moyo. [Fotokozani m’mawu anuanu ndime 1 ndi 2 patsamba 6 m’brosha la Chifuno cha Moyo.] Chivumbulutso 4:11 chikufotokoza kuti Yehova Mulungu ndiye Mlengi wathu. [Ŵerengani.] Ndithudi ayenera kuti anali ndi chifukwa chotilengera. Anthu amene afuna kuchidziŵa aphunzira Mawu olembedwa a Mulungu, Baibulo. Ndikufuna kukupatsani mwaŵi umenewo.” Fotokozani mmene timachititsira phunziro lathu la Baibulo lapanyumba, ndipo konzani kuti mudzayambe phunzirolo.

6 Mafikidwe abwinowa angatonthoze awo amene wokondedwa wawo wamwalira:

◼ “Ndikuthandizana ndi onse amene wokondedwa wawo wamwalira. Popeza chimenechi chingakhale chimodzi mwa zinthu zovuta koposa kwa ife kupirira, broshali, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, lakonzedwa. Lathandiza mamiliyoni a anthu. Ndikufuna kukusonyezani zimene limanena pa lonjezo losangalatsa limene Yesu Kristu anapereka. [Ŵerengani ndime yachisanu patsamba 26, kuphatikizapo Yohane 5:21, 28, 29.] Taonani chithunzichi patsamba 29 chosonyeza nkhani ya Uthenga Wabwino ya Yesu akuukitsadi Lazaro kwa akufa. Ngati mungakonde kuliŵerenga brosha lotonthozali, nditha kukusiyirani pachopereka cha K3.60.”

7 Mutabwererako, mungasonyezenso chithunzi cha patsamba 29 la brosha lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira” ndi kunena kuti:

◼ “Kumbukirani zimene tinakambitsirana ponena za Kristu kuti anaukitsa Lazaro kwa akufa. [Ŵerengani mawu ofotokoza chithunzi patsamba 28, ndipo kambitsiranani nkhani ya pamutu waung’ono wakuti “Kodi Zinachitikadi?”] Ngati mtima wanu ukukhumba kuonanso wokondedwa wanu amene anamwalira, ndiloleni ndikuthandizeni kupanga chiyembekezo cha chiukiriro kukhala chanuchanu.” Pemphani kumchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba.

8 Tiyeni tichite zonse zimene tingathe m’miyezi ikudzayi kutsanzira Yesu mwa ‘kutonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’—Yes. 61:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena