Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/94
  • Mbali ya Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbali ya Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 9/94

Mbali ya Mafunso

◼ Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ndi malipoti a maphunziro a Baibulo mlembi atakonza lipoti lamwezi ndi mwezi la utumiki wakumunda?

Mlembi ayenera kusunga malipoti a maphunziro a Baibulo m’bokosi lake losungiramo lanthaŵi zonse kwa miyezi iŵiri; pambuyo pake, malipoti a maphunzirowo angaperekedwe kwa ochititsa Maphunziro Abuku Ampingo amene adzawapeza kukhala othandiza popereka chilimbikitso ndi chithandizo chaumwini kwa ofalitsa amene akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Chithandizo chingaperekedwenso kwa anthu amene akuphunzirawo.

Ochititsa maphunziro abuku ayenera kuyesayesa kudziŵana ndi anthu okondwerera ndi kuwalimbikitsa kusonkhana ndi kagulu ka phunziro labuku lakumaloko, ngati nkotheka. Wochititsa phunziro angakambitsirane molimbikitsa ndi abale ndi alongo ponena za maphunziro awo a Baibulo apanyumba, mwinamwake mwa kugwiritsira ntchito nthaŵi yokhalapo misonkhano yanthaŵi zonse ya mpingo isanayambe kapena pambuyo pake. Iye angakhozenso kulinganiza kutsagana ndi ofalitsa ena ku maphunziro awo a Baibulo apanyumba ndi kupereka chilimbikitso chauzimu mwanjira imeneyo. Ndiponso woyang’anira utumiki angapereke chilimbikitso ponena za ntchito ya phunziro la Baibulo lapanyumba pamene akuchezera gulu la Phunziro Labuku Lampingo, akumagwiritsira ntchito mawu operekedwa pa lipoti la phunziro la Baibulo lapanyumba.

Faelo ya mlembi ya malipoti a maphunziro a Baibulo iyenera kuperekedwa kwa woyang’anira dera pamene achezetsa mpingo. Iye angakhozenso kutsagana ndi ofalitsa ena pamene akukachititsa maphunziro awo a Baibulo apanyumba. Zimenezi ziyenera kukhaladi zolimbikitsa makamaka kwa wophunzira ndi zothandiza kwa munthu wochititsa phunzirolo. Mwinamwake woyang’anira dera angakhoze kufikira ena a anthu okondwerera ameneŵa panthaŵi ina mkati mwa kuchezera kwake.

Nthaŵi iliyonse pamene phunziro la Baibulo liimitsidwa, zimenezi ziyenera kulembedwa pa silipi la lipoti la phunziro la Baibulo, chifukwa chake chikumasonyezedwa. Pamene woyang’anira dera achezera mpingo, adzapenda malipoti a phunziro la Baibulo. Zingachitike kuti ena amene aimitsa maphunziro awo angathe kuthandizidwa kuti azindikire mokulirapo za zosoŵa zawo zauzimu. Kukakhala kwabwino kwambiri chotani nanga ngati maphunziro ena oimitsidwa angayambitsidwenso ndipo anthuwo nathandizidwanso mwauzimu!

Tonsefe tili okondweretsedwa kwambiri ndi ntchito ya kupanga ophunzira ndipo tidzafuna kugwiritsira ntchito mpata uliwonse kulimbikitsa ndi kuthandiza atsopanowo amene akuyamba kudziŵa choonadi. Malipoti a phunziro la Baibulo lapanyumba angathandize. Wochititsa Phunziro Labuku Lampingo akhoza kutaya masilipi a malipoti akalewo mwezi ndi mwezi pamene alandira atsopano kuchokera kwa mlembi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena