Nyimbo 76
Yehova, Bwenzi Lathu Labwino Kopambana
1. Yehova Wodalirika,
Ndibwenzi lathudi.
Anapanga dziko lathu,
Napereka moyo.
Makolowo anakana
Njira ya Yehova,
Ali bwenzi la omvera
Ofuna tsikulo.
2. Munthu wokhulupirika
Ndiye Abrahamu.
Yehova atamuyesa,
Iye sanasinthe.
Anadziŵa kuti mwana
Wake adzauka.
Ya anakonda Abra’mu,
Wosunga umphumphu.
3. Yesu anadza kudziko
Chifukwa cha anthu.
Anatitayira moyo
Kutiyanjanitsa.
Satana anayesadi
Kupatutsa Yesu,
Monga wokhulupirika,
Anali wowona.
4. Palibe bwenzi loposa
Yehova ndi Kristu.
Anasonyeza chikondi
Chopezetsa moyo.
Ubwenzi ndi dziko ndiwo
Udani ndi M’lungu.
Tisonyezedi kukhala
Mabwenzi owona.