Zilengezo
◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu November: New World Translation of the Holy Scriptures ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. January: Lililonse la mabuku a masamba 192 otsatirawa amene mpingo ungakhale nawo m’sitoko pa 50t lililonse: Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu; Commentary on the Letter of James; Is the Bible Really the Word of God?; Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?; Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo; Life Does Have a Purpose; Mbiri Yabwino Yokusangalatsani ndi Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo. MUSAODE alionse a mabuku ameneŵa m’Chingelezi ku Sosaite popeza kuti mulibe m’sitoko. Komabe, Sosaite ili ndi mtokoma wochepa wa buku la Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo m’Chicheŵa ndipo ameneŵa angaodedwe. Ngati mipingo ilibe alionse a mabuku otchulidwa pamwambapa m’sitoko, ingagaŵire Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? February: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Bukuli litagaŵiridwa payenera kukhala maulendo obwereza, ndipo muyenera kuyesayesa kuyambitsa phunziro la Baibulo. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapa iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Order (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Tikufuna kulimbikitsa olembetsa, kumene kuli kotheka, kugwiritsira ntchito keyala ya mpingo kotero kuti masabusikripishoni ochuluka azitumizidwa ndi lole m’malo mwa kutumiza papositi.
◼ Zofalitsidwa Zimene Zilipo:
Chicheŵa: Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona. Chingelezi: Learn to Read and Write; Revelation—Its Grand Climax At Hand!
◼ Makaseti Amene Alipo:
Alubamu ya Hebrew Scriptures Volume I (Genesis mpaka Rute); Alubamu ya Hebrew Scriptures Volume III (Miyambo mpaka Malaki). (Amachita K150.00 imodzi kwa ofalitsa ndi K100.00 kwa apainiya.)