Misonkhano Yautumiki ya November
Mlungu Woyambira November 7
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani mfundo imodzi kapena ziŵiri zokambitsirana m’magazini alionse atsopano zimene zingagwiritsiridwe ntchito powagaŵira.
Mph. 18: “Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za kufunika kwa kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse zozikidwa pa mawu oyamba a Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1994.
Mph. 17: “Baibulo—Magwero a Chitonthozo ndi Chiyembekezo m’Dziko la Mavuto.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino zosonyeza mmene maulaliki osonyezedwawo angagwiritsidwire ntchito.
Nyimbo Na. 24 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 14
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Ŵerengani lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro zilizonse za zopereka. Tchulani makonzedwe a utumiki wakumunda a pakutha kwa mlungu.
Mph. 17: “Kodi Mumasonyeza Mzimu Wotani?” Nkhani. Phatikizanipo mawu otengedwa m’kope la Nsanja ya Olonda ya December 15, 1977, tsamba 561, ndime 4 ndi 5.
Mph. 18: “Njira Zowongolera Ulaliki Wathu wa Ufumu.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zosonyeza mmene malingaliro operekedwa mu Utumiki Wathu Waufumu agwiritsidwira ntchito ndi zotulukapo zabwino.
Nyimbo Na. 37 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 21
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Bokosi la Mafunso. Nkhani. Igwirizanitseni ndi mkhalidwe wakumaloko.
Mph. 15: Zosoŵa za pamalopo. Kapena nkhani yokambidwa ndi mkulu ya mutu wakuti “Yamikirani Utumiki Wanu Wopatulika,” m’kope la Nsanja ya Olonda ya September 1, 1994, tsamba 29.
Mph. 18: “Athandizeni ‘Kudzamvanso.’” Kambitsiranani ndi omvetsera. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino zosonyeza mmene Baibulo lingagwiritsidwire ntchito poyambitsa phunziro.
Nyimbo Na. 52 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 28
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Sonyezani njira zogaŵirira magazini atsopano.
Mph. 17: “Madalitso a Kugwira Ntchito ndi Ena.” Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani onse kuchirikiza misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda yolinganizidwa ndi mpingo mmalo mwa kupanga makonzedwe aumwini nthaŵi zonse a kupita mwa iwo okha. Kugwira ntchito ndi kagulu kumadzetsa madalitso owonjezereka, utumiki wogwira mtima kwambiri, ndi kulimbikitsana.
Mph. 18: Kugaŵira Buku la Munthu Wamkulu m’December. Buku limeneli likufunikira kwambiri. Mamiliyoni mazana ambiri a anthu amanena kuti ali otsatira a Yesu ndipo amanena kuti amakhulupirira zimene iye anaphunzitsa. Anthu afunikira kudziŵa zimene zinamsiyanitsa iye ndi anthu ena onse—chipulumutso chawo chimadalira pa zimenezo. Buku la Munthu Wamkulu, m’mutu 133, limati: “Mitima yathu imasonkhezeredwa pamene tilingalira kulimba mtima kwake kwakukulu ndi uchamuna, nzeru zake zosayerekezereka, luso lake lopambana monga mphunzitsi, utsogoleri wake wopanda mantha, ndi chikondi chake chopanda mpeni kumphasa ndi chifundo.” Baibulo limamdziŵikitsa bwino lomwe monga (1) Mboni (Yoh. 18:37), (2) Mpulumutsi (Mac. 4:12), ndi (3) Mfumu (Chiv. 11:15). Khalani ndi wofalitsa wokhoza asonyeze ulaliki akumagwiritsira ntchito zina za mfundo zimenezi. Limbikitsani onse kukhala ndi phande m’kugaŵira buku limeneli m’December.
Nyimbo Na. 61 ndi pemphero lomaliza.