Nyimbo 52
Dzina la Atate Wathu
1. Yehova inu Wamkulu,
Yeretsani dzina lo.
Muchite chifuno chanu,
Lileke kudetsedwa.
Lidzayeretsedwa msanga,
Mwa chilakiko chanu.
Kulitsani mbiri yanu;
Onse alabadire.
(Korasi)
2. Tifunanso kuyeretsa
Dzina lanu loyera;
Tilankhula molimbika
Za zifuno zanuzo.
Mwa kukhulupiriraku,
Tikulemekezani.
Tikhulupiriketu kwa
Atate Woyeranu.
(Korasi)
3. O Ambuye Yehovanu,
Ndinu Wammwambamwamba.
Palibe china choposa
Kukulemekezani.
M’dzina lanu timaguba;
Tifuna kusonyeza
Kuti ndinu wa chifuno
Mudzadalitsidwadi.
(KORASI)
Mfumu ndinu Mpangi wathu;
Chilengedwechi nchanu,
Poti ndinu Mulungudi
Wokwanitsa zifuno.
Yehova munapereka
Mwana wanu wayekha,
M’chite chifuniro chanu,
Padziko lapansili.