Nyimbo 18
Dalitsani Ubale Wathu Wachikristu
1. Kristu mokomadi
Anaphunzitsatu,
Ophunzira ake
Napatsa mtendere.
Anasonyeza chikondi,
Cha chilungamocho,
Nasonyeza kudekha ndi
Chikondi chowona.
(Korasi)
2. Akristu akondwa
Omvera Yehova!
Ofatsa adala,
Omvera Mulungu!
Ophunzira a Yesuwo
Akonda ubale,
Amalengeza Ufumu
Pamodzi mokondwa.
(Korasi)
3. Timke ndi mbiriyo
Kwa onse ofuna,
Athandizenitu
Kusankha Mulungu.
Muwathandize kumfuna,
Adakapezeka,
Agwirizane Mu’bale,
Kuti akondwere.
(KORASI)
Titama inu Ya;
Mulidi wabwino.
O Atate wakumwamba,
M’dalitse ubale wathu.