Nyimbo 25
Zinthu Zabwino za Mulungu
1. M’lungu anapanga
Zinthu m’nthaŵi yake.
Kudya, kumwa, ntchito,
Izitu ndimphatso.
Waika zosatha
Mumitima yathu.
Ndi chiyembekezo
Cha moyo wosatha.
2. Yehova afuna
Kupatsa anthufe
Madalitso zedi
Kuti timkondebe.
Anthu adzakhala
Ndi zinthu zabwino;
Nadzakhala ndi
Ya Kunthaŵi yosatha.
3. Ntchito yaikulu
Yomwe taphunzira
Ndiyolalikira;
Timaisamala.
Ndimphatso ya M’lungu
Idzetsa chimwemwe.
Nkanthu kabwinodi
Komwe tili nako.
4. Tikhale anzeru
Mumasiku onse
Tinene za M’lungu
Tichite zabwino.
Ilitu ndigawo
Lomwe tikusankha,
Tichita zonsezi
Ka’mba ka Yehova.