Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/94
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisamala Mukakhala mu Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 11/94

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi tifunikira kukhala ochenjera motani pogwira ntchito m’gawo lowopsa?

1 Timamva malipoti owonjezerekawonjezereka a chiwawa, kuukiridwa, ndi zipolowe m’chitaganya, makamaka m’matauni. Ngakhale kuti timada nkhaŵa, tidziŵa kuti ngakhale m’madera azipolowe, muli anthu oona mtima amene angalabadire uthenga wa Ufumu. Chotero panthaŵi yoyenera, tiyenera kulimba mtima kupitabe patsogolo, tili ndi chidaliro chakuti Yehova adzatisamalira.—Miy. 29:25; 1 Ates. 2:2.

2 Pamene tipita m’dera looneka kukhala lowopsa, Yehova amafuna kuti tikhale ochenjera ndi kugwiritsira ntchito kuweruza kwabwino. Khalani atcheru. “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miy. 22:3) Ofalitsa ozoloŵera amazindikira nzeru ya kugwirira ntchito pamodzi ali aŵiriaŵiri kapena ngakhale m’timagulu ta ofalitsa angapo, ngati kuli kofunikira. Mlaliki 4:9, 12 amati: “Aŵiri aposa mmodzi . . . Ndipo wina akamlaka mmodziyo, aŵiri adzachirimika.” Kaŵirikaŵiri apandu amafuna amene ali okha amene samavuta kuukira.

3 Samalani kwambiri poloŵa m’nyumba zosanja zokhala ndi malikole amdima ndi makwerero opanda anthu. Chenjerani pamene mwaitanidwa kuloŵa m’nyumba kapena m’chipinda. Musakangane ndi amene angakhale akukuwopsani kapena kukutokosani. Fulumirani kudzidziŵikitsa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Ofalitsa ena nthaŵi zonse amakhala ndi Baibulo kapena magazini a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! kumanja zowadziŵikitsa.

4 Yang’anirani anthu omwe akungoyendayenda m’deralo. Samalani za kuloŵa m’chikepe ndi ena amene sakuoneka kuti amakhala m’nyumbayo. Musavale zokometsera zokwera mtengo. Ngati mudzatulukira kutada, peŵani kuyenda m’makwalala amdima amene ali ndi anthu ochepa. Ngati mwaukiridwa, musalimbane naye ngati angofuna ndalama kapena zinthu zina zimene muli nazo; moyo wanu uposa chinthu chilichonse chakuthupi chimene muli nacho.—Marko 8:36.

5 Abale amene akutsogolera afunikira kukhala atcheru, akumadziŵa kumene ofalitsa ali ndi zimene akuchita m’gawolo. Kaŵirikaŵiri kuli bwino koposa kuti kagulu kakhale m’dera limodzi kotero kuti ena azikhala pafupi nthaŵi zonse. Ngati m’malowo mwabuka chipolowe kapena chiwawa chilichonse, kaguluko kayenera kuchoka m’gawolo mwamsanga.

6 Ngati tikhala atcheru ndi ochenjera, tingapitirize kufikira awo okhala m’madera mmene upandu uli wofala amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa.”—Ezek. 9:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena