Athandizeni ‘Kudzamvanso’
1 “Tidzakumvanso za chimenechi.” (Mac. 17:32) Nzimene ena ananena atamvetsera nkhani yotchuka ya Paulo pa phiri la Mars. Lerolinonso, ena ali ofunitsitsa kumva zowonjezereka za uthenga wa Ufumu umene tinakambitsirana nawo paulendo wathu woyamba.
2 Mbali yaikulu ya kuphunzitsa timaichita pamene tibwerera kukakulitsa chikondwerero. Kukonzekera kwabwino kudzatithandiza kupeza zotulukapo zabwino. Bukhu Lolangiza la Sukulu patsamba 51 limalangiza kuti: “Choyamba chititsani zigomeko zochirikiza nkhaniyo kukhala zomvekera bwino m’maganizo. Yesani kudziŵa chifukwa chake kanthu kena kaliri motero. Onani ngati mungathe kunena malingalirowo m’mawu anuanu. Zindikirani bwino lomwe maumboni Amalemba. [Khalani wokonzekera kugwiritsira ntchito malemba mogwira mtima.]”
3 Ngati munagaŵira buku lakuti “Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?,” munganene zonga izi:
◼ “Pamene tinalankhuzana tsiku lija, tinakambitsirana zifukwa zimene tingakhalire ndi chidaliro pa Baibulo. Buku limene ndinakusiyirani limapereka funso lakuti, ‘Kuŵerengeranji Baibulo?’ [Ŵerengani mawu oyamba patsamba 5, ndi kuyembekezera yankho pa funso lomalizira.] Baibulo limatiuza kuti posachedwapa Mulungu mwiniyo adzathetsa mavuto onse othetsa nzeru mtundu wa anthu, ndipo limatitsogolera m’njira imene tiyenera kuyendamo kuti tikalandire madalitso a nthaŵi yachisangalalo imeneyo. [Ŵerengani Salmo 119:105.] Bukuli linakonzedwa kukhala lothandizira phunziro la Baibulo laumwini ndi la banja. Ndikufuna kukusonyezani mmene mungaligwiritsirire ntchito.”
4 Kwa amene munasiyira trakiti lakuti “Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo,” munganene kuti:
◼ “Tonsefe timafuna kudziŵa zimene zili mtsogolo. Poona mikhalidwe yadziko ya lerolino, kodi muganiza kuti nchiyani chimene chidzachitika? [Yembekezani yankho.] Pamene kuli kwakuti munthu angangoganizira chabe za zimene zidzachitika, Mulungu amadziŵa bwino lomwe chimene chidzachitika. [Ŵerengani Yesaya 46:10.] Mungadabwe kudziŵa kuti Baibulo limaneneratu kuti posachedwapa tidzasangalala ndi madalitso a dziko latsopano la paradaiso. [Ŵerengani ndime yachitatu patsamba 4.] Lekani ndikuuzeni zowonjezereka ponena za lonjezo labwino koposa limeneli.”
5 Ngati mukubwerera kumene munagaŵira “New World Translation,” mwinamwake njira iyi ingagwire ntchito kwa inu:
◼ “Posachedwapa, ndinakusiyirani Baibulo, ndipo ndinalonjeza kubweranso kudzakuthandizani mmene mungapindulire nalo koposa. Nthaŵi zina tingalingalire kuti ndimotani mmene tingasungire unansi waubwenzi ndi ena. Baibulo limapereka uphungu wabwino, ndipo New World Translation imasonyeza njira yosavuta yopezera zimene tifunikira. [Tsegulani patsamba 1595 ndi kuona pansi pa mutu wakuti “Love(s).” Sonyezani malemba onga 1 Akorinto 13:4; Akolose 3:14; ndi 1 Petro 4:8. Fotokozani mwachidule mmene kugwiritsira ntchito mikhalidwe imeneyi kungatulutsire zipatso zabwino.] Ichi nchitsanzo chimodzi chabe chosonyeza mmene Baibulo limaperekera mayankho okhutiritsa pa mavuto athu. Paulendo wotsatira, ndidzafuna kukusonyezani njira ina imene Baibulo lingatithandizire kupeza chimwemwe ndi mtendere wa maganizo.”
6 Palibe chuma chamtengo wapatali chimene tingagaŵire ena choposa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu. Chidziŵitso choterocho chingaphunzitse anthu kuwopa Yehova ndi kuwalimbikitsa kuyenda m’njira yake, imene imadzetsa madalitso osatha.—Miy. 2:20, 21.