Baibulo Nlimene Mulungu Amatsogozera Anthu Onse
1 Pafupifupi Ma Baibulo Mamiliyoni Zikwi Zinayi Asindikizidwa M’zinenero 2,100, Kuti Mawu A Mulungu Afike Kwa Anthu Oposa 90 Peresenti Mwa Anthu Onse Okhala Padziko Lapansi. Komabe, Padziko Lapansi Pali Njala “Ya Kumva Mawu A Yehova.” (Amosi 8:11) Anthu Ambiri Amene Ali Ndi Baibulo Mwina Samaliŵerenga Kapena Samalimvetsetsa. Kodi Tingawasonkhezere Bwanji Kuti Azigwiritsira Ntchito Baibulo Kuti Liziwatsogoza M’moyo Wawo?
2 Mu December Muno Tizigaŵira Buku Lakuti, Baibulo—kodi Ndilo Mawu A Mulungu Kapena A Munthu? Tidzakhala Tikusonyeza Kuyamikira Kwathu Mphatso Imeneyi Yochokera Kwa Yehova Pothandiza Ena Mwachimwemwe Kukhulupirira Baibulo Kuti Nlimene Mulungu Amatsogozera Anthu Onse.
3 Mungayambe ulaliki wanu mogwiritsira ntchito trakiti lakuti “Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo.” Munganene kuti:
◼ “Anthu oposa 90 peresenti mwa anthu onse okhala padziko lapansi ali nalo Baibulo, koma ngoŵerengeka okha amene amaliŵerenga nthaŵi zonse. Mukuganiza kuti chifukwa chake nchiyani?” Ŵerengani ndime ziŵiri zoyamba za trakitiyo, limodzi ndi 2 Timoteo 3:16. Ndiyeno gaŵirani buku lakuti Mawu a Mulungu pa chopereka cha K12.00. Mpempheni mwini nyumbayo kuti aŵerenge trakiti yonseyo. Fotokozani kamutu kotsirizira kakuti, “Kuneneratu Zamtsogolo.”
4 Mutabwerera kwa anthu amene munasiyira trakiti yakuti “Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo,” mungayese izi:
◼ Mutadzidziŵikitsanso, ŵerengani ndime ziŵiri zotsirizira za trakitiyo. Mfunseni mwini nyumbayo ngati anaganizapo zoti nkotheka kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Atayankha, nenani kuti: “Mboni za Yehova sizimakayikira kuti maulosi onse omwe ali m’Baibulo adzakwaniritsidwa, kuphatikizapo amene amaneneratu kuti anthu onse amene amakwanitsa zofuna za Mulungu adzakhala ndi mtsogolo mosangalatsa.” Sonyezani chithunzi chili patsamba 13 mu brosha lakuti Mulungu Amafunanji, bwererani paphunziro 5, ndipo kambitsiranani mayankho a mafunso amene andandalikidwa pamenepo, mmene mukuteromo, mwayamba phunziro.
5 M’dera limene anthu ake ngokonda chipembedzo, mungayese kuyamba kuwafikira motere:
◼ “Tikulimbikitsa anthu kuti azilemekeza Baibulo kwambiri. Mabanja ambiri ali nalo Baibulo, koma si kwenikweni kuti amaliŵerenga pamene ali ndi mavuto aakulu. Kodi zimenezo mwaziona? [Yembekezerani yankho.] Kapena amaganiza kuti Baibulo nlakale. Buku lino, lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, likupereka umboni wogwira mtima wakuti Baibulo limanena zasayansi molondola ndipo limapereka mayankho othandiza pamavuto othetsa nzeru a leroŵa.” Sonyezani mfundo zingapo m’mutu 8 kapena m’mutu 12 wa bukulo, kenako ligaŵireni.
6 Pamene mwabwerera kumene munasiya buku lakuti “Mawu a Mulungu,” munganene kuti:
◼ “Pamene ndinakuchezerani poyamba paja, tinakambitsirana za mmene Baibulo limathandizira kuthetsa mavuto aakulu a leroŵa. Amene alikhulupirira kuti ndi Mawu a Mulungu athandizidwanso kukhala ndi moyo wachimwemwe ndipo wokhutiritsa kwambiri. Ndingakonde kukusonyezani limodzi la mapulinsipulo othandiza a m’Baibulo amene afotokozedwa m’buku ndinakusiyirani lija.” Kambitsiranani limodzi la mapulinsipulo a m’Malemba pamutu 12, ndime 3-6, ndiye malizani mwa kuŵerenga ndime 7. Ngati wasonyeza chidwi, mpempheni kuphunzira naye buku la Chidziŵitso kapena brosha lakuti Mulungu Amafunanji.
7 Ulaliki wotsatirawu ungachititse chidwi anthu achikulire:
◼ “Kale anthu ambiri anali kuŵerenga Baibulo ndipo mabanja ankagwiritsira ntchito mapulinsipulo ake. Kodi inunso m’banja lanu zinali choncho? [Yembekezerani yankho.] Lerolino kukuoneka kuti ambiri ngotanganidwa kwenikweni moti samapeza nthaŵi yoŵerenga Baibulo kapena amaganiza kuti mapulinsipulo ake ophunzitsa khalidwe ngachikale. Mutu 13 wa buku lino lakuti, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, ukufotokoza zochitika zenizeni zitatu za anthu amene miyoyo yawo inasintha nkukhala yabwino ataphunzira Baibulo. Ngati mungakonde kuŵerenga mmene mphamvu ya Mawu a Mulungu inawathandizira, ndingakondwe kukusiyirani buku limeneli pa chopereka cha K12.00.”
8 Paulendo wobwereza, munganene kuti:
◼ “Pamene tinacheza poyamba paja, tinavomerezana kuti lero anthu amanyalanyaza mapulinsipulo a Baibulo ophunzitsa khalidwe. Kodi kunyalanyaza kwawoko kuyenera kutikhudza? [Yembekezerani yankho.] Yesu Kristu ananena kuti nkofunika kwenikweni kulidziŵa Baibulo.” Ŵerengani Yohane 17:3. Ndiyeno ŵerengerani pamodzi ndime 5 ya mutu 1 m’buku la Chidziŵitso. Fotokozani za programu yathu yaphunziro la Baibulo laulere, ndipo mpempheni nthaŵi yomweyo kumsonyeza mmene timachitira.
9 Pempherani kuti Yehova akudalitsireni khama lanu pozindikiritsa anthu kuti Baibulo nlimene Mulungu amatsogozera anthu onse.