Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
1 Musanadziŵe choonadi molongosoka, mwina munali ndi mafunso ambiri onena za moyo amene munalephera kuyankha. Ndiye munakondwa chotani nanga pamene munalandira mayankho a Baibulo a mafunso amenewo! Tsopano mungathandize enanso kupeza mayankho ofananawo. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:2.) Mungawauze choonadi chonena za Mulungu chotsogolera ku moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Komano mungamthandize bwanji wina kuzindikira kufunika kwa chidziŵitso chimenechi? Chabwino, tangoganizani za mafunso amene choonadi chinakuyankhirani. Kodi amene akufunafuna choonadi akufuna kudziŵanji? Kuganiza zimenezo kungakuthandizeni kugaŵira buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Malingaliro otsatiraŵa angakuthandizeni pokonzekera kuchitira umboni m’June.
2 Popeza anthu ambiri amadabwa chifukwa chake padziko lapansi pali mavuto ochuluka chotere, wina angachite chidwi mutayamba chonchi:
◼ “Pamene kwagwa tsoka kapena pamene upandu ndi chiwawa zikuwonjezeka, kaŵirikaŵiri anthu amafunsa chifukwa chake zinthu zoipazi zikuchitika. Kodi inuyo mungayankhe bwanji?” Yembekezerani ayankhe ndipo yamikirani yankho lake. Kenako pitani pa mutu 8 m’buku la Chidziŵitso, ndipo msonyezeni zimene lafotokoza m’ndime 2. Fotokozani kuti buku limeneli likulongosola mmene Baibulo limafotokozera chifukwa chake zinthu zoipa zikuchitika, ndipo nenani kuti: “Ndingakonde kukusiyirani buku limeneli pa chopereka cha K12.00.”
3 Pamene mwabwerera kumene munasiya buku la “Chidziŵitso”, munganene kuti:
◼ “Ndinachita chidwi ndi zimene munanena kuti ndizo zikuchititsa mavuto ambiri choncho padziko lapansi. Kodi mukugwirizana nalo yankho la Baibulo limene laperekedwa m’bukuli?” Yembekezerani yankho. Ŵerengani ndime 17 patsamba 77 m’buku la Chidziŵitso, ndipo pemphani kuŵerenga Aroma 9:14 m’Baibulo la mwini nyumbayo. Ndiyeno nenani kuti: “Sikuti Mulungu amativulaza ndi kutivutitsa mosayenera iyayi. Walonjeza kutipatsa moyo wosatha mumtendere ndi chimwemwe. Mutu woyamba m’buku lino umati ‘Mungathe Kukhala ndi Mtsogolo Mwa Chimwemwe!’ Ndingakonde kukusonyezani mmene zimenezo zingakhalire zenizeni kwa inu ndi okondedwa anu.” Pitani pamutu 1, ndi kusonyeza mmene timaphunzirira. Ngati mkhalidwewo ukulola phunzirani chigawo chokulirapo cha mutuwo.
4 Mwina mungakonde kugwiritsira ntchito mawu oyamba ali patsamba 13 m’buku la “Kukambitsirana” pamutu wakuti “Ukalamba/Imfa”:
◼ “Kodi munafunsapo kuti, ‘Kodi imfa ndiyo mapeto a zonse?’ Kapena kodi pali kanthu kena pambuyo pa imfa? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limayankha funso lililonse limene tingakhale nalo ponena za imfa. [Ŵerengani Mlaliki 9:5, 10.] Limasonyezanso kuti pali chiyembekezo chenicheni kwa amene ali ndi chikhulupiriro. [Pitani pa ndime 13 patsamba 84 m’buku la Chidziŵitso; ŵerengani ndi kufotokoza mawu a Yesu ali pa Yohane 11:25.] Mutu wonsewu ukuyankha funso lakuti, Kodi nchiyani chimachitika kwa okondedwa athu akufa? Ngati mungakonde kuliŵerenga, ndingakusiyireni buku limeneli pa chopereka cha K12.00.”
5 Pamene mwabwererako, mungakumbutsanenso maina ndi kunena kuti:
◼ “Ulendo uja tinakambitsirana za chimene chimachitika munthu akafa. Anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu alionse pambuyo pa imfa amapita kumwamba kapena kuhelo. Koma kodi munalingalirapo zoti kungatheke kuti akufa adzakhalenso ndi moyo pompano padziko lapansi? [Yembekezerani yankho.] Malinga ndi Baibulo, oukitsidwawo adzakhala pamodzi ndi ofatsa omwe adzalandira dziko lapansi. [Ŵerengani Salmo 37:11, 29, ndiyeno kambitsiranani ndime 20 patsamba 88 m’buku la Chidziŵitso.] Chiyembekezo chimenecho chatonthoza anthu mamiliyoni ambiri amene anali kuopa imfa, ndipo akhala ndi cholinga chabwino. Bukuli likuthandizani kuimvetsetsa bwino nkhaniyo. Kodi ndingakusonyezeni?”
6 Ngati mukufuna ulaliki wosavuta, tayesani uwu:
◼ “Ndikufuna kukusonyezani chithunzi china m’buku ili lakuti, Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Nchithunzi chokongola, eti?” Litseguleni bukulo moti mwini nyumbayo aone masamba 4-5. Yembekezerani yankho. Ndiyeno ŵerengani mawu ali patsamba 5. Malizani mwa kunena kuti: “Mungatsale nalo bukuli kuti muliŵerenge nokha. Ndi K12.00 basi.” Onani imene ingakhale nthaŵi yabwino yobwererako kukakulitsa chidwi chimene wasonyeza.
7 Tili ndi chidziŵitso chochokera kwa Mulungu choyankha mafunso ofunika ponena za moyo. Konzekerani bwino, ndipo Yehova adzadalitsa khama lanu pouza ena chidziŵitso chopatsa moyo chimenechi amene akufunafuna choonadi.