Sungani
Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
Gwiritsani ntchito mfundo zotsatirazi kukuthandizani kukonzekera maulaliki a mmene mungagawire mabuku ogawira mwezi umenewo.
Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
“Tikukhala mu nthawi imene pafupifupi aliyense akukumana ndi mavuto. Ambiri amafufuza malangizo kwa alangizi osiyanasiyana. Ena amakafufuza kwa asing’anga a mizimu. Kodi mukuganiza n’kuti kumene tingapeze malangizo abwino amene tingagwiritse ntchito? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena mfundo yothandiza kwambiri imene tonsefe tiyenera kuidziwa. [Werengani 2 Timoteo 3:16. Ndiyeno tsegulani patsamba 187, ndipo werengani ndime 9.] Buku ili lidzakuthandizani kuzindikira mmene kutsatira zimene Baibulo limanena nthawi zonse kumakhalira kothandiza.”
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha
“Ngati akanakupemphani kuti mukakhale m’malo okongola ngati awa, kodi mukanavomera? [Muonetseni chithunzi cha patsamba 4 ndi 5, ndipo yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Mawu a Mulungu akunena pa zimene tingachite kuti tidzasangalale ndi moyo woterewu kosatha. [Werengani Yohane 17:3.] Buku ili lidzakuthandizani kupeza chidziwitso chotsogolera ku moyo wosatha.” Konzani zodzakambirana ndime 5 zoyambirira za mutu 1 pa ulendo wotsatira.
Tsegulani chithunzi cha patsamba 188 ndi 189, n’kugwiritsa ntchito mawu amene ali pamenepowo kufunsa mwininyumba kuti: Kodi mufuna kudzakhala ndi moyo m’paradaiso pamene chidziwitso chonena za Mulungu chidzaza dziko lapansi? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Yesaya 11:9.] Buku ili lidzakuthandizani kuphunzira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Paradaiso ndi mmene ifeyo tingadzakhalire m’Paradaiso ameneyo.” Konzani zodzakambirana ndime 11 mpaka 16 za mutu woyamba pa ulendo wotsatira.
Dikirani!
“Anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa cha mavuto aakulu ndi zochitika zoopsa zimene zafala masiku ano. [Tchulani chitsanzo chodziwika bwino m’dera lanulo.] Kodi mukudziwa kuti zimene zikuchitikazi padziko lonse ndi chizindikiro chosonyeza kuti boma la Mulungu posachedwapa liyamba kulamulira dziko lapansi? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani lemba loyenerera, monga ngati Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:7, 10, 11; kapena 2 Timoteo 3:1-5.] Kabuku aka kakufotokoza chifukwa chake panopa tiyenera kukhala maso kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitikazi.”
“Anthu ambiri masiku ano akuvutika maganizo ndi zinthu zoopsa zimene zikuchitika m’dzikoli kapena zimene zawachitikira. Ena amadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu salowererapo kuti aletse zinthu zimenezi. Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa zopweteka zonse zimene zikuvutitsa anthu. [Werengani Chivumbulutso 14:6, 7.] Taonani zimene zidzachitikira anthu Mulungu akadzapereka chiweruzo. [Werengani 2 Petro 3:10, 13.] Kabuku aka kakufotokoza zambiri pa nkhani yofunika kwambiri imeneyi.”
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu anafuna kuti tizikhala m’mavuto ngati amene tikukumana nawo masiku anowa? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Mateyu 6:10.] Kodi munayamba mwaganizapo kuti kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani kwenikweni?” Pitani pa mutu 6, ndipo werengani mafunso amene ali koyambirira kwa phunzirolo. Mungayambe kukambirana phunzirolo kapena mungakonze zodzakambirana pa ulendo wotsatira.
“Ngakhale kuti zinthu m’dzikoli zikupita patsogolo, matenda ndi imfa zikupitirizabe kusautsa anthu. Kodi mukudziwa zimene Yesu adzachite kwa odwala, okalamba, ngakhale akufa?” Yembekezani ayankhe. Ngati munthuyo akufuna kuti adziwe yankho lake, tsegulani phunziro 5, ndi kuwerenga mafunso a ndime 5 ndi 6. Kambiranani ndimezo kapena, konzani zodzakambirana pa ulendo wotsatira.
Lambirani Mulungu Woona Yekha
“Kodi mukuganiza n’kuti kumene tingapeze thandizo pa mavuto a moyo wathu? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Aroma 15:4.] Taonani kuti Malemba ouziridwa amatipatsa malangizo, chitonthozo, ndi chiyembekezo, zimene zikhoza kutilimbikitsa kupirira mavuto. Buku ili likupereka mfundo zabwino za mmene kuwerenga Baibulo kungatithandizire.” Tchulani mfundo 4 zimene zili patsamba 30.
“Kuchokera pamene Yesu anali pano padziko lapansi, anthu ambiri akhala akupempherera Ufumu wa Mulungu kuti udze. Kodi munayamba mwaganizapo kuti kodi Ufumu umenewu ukabwera anthu zidzawakhalira bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Danieli 2:44.] Buku ili likufotokoza kuti kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, zimene udzachite, ndiponso mmene tingapindulire ndi ulamuliro wake wolungama.” Sonyezani chithunzi chimene chili patsamba 92 ndi 93.
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
“Nthawi ino anthu ambiri akuganiza za Yesu. Komabe, popeza kuti zinthu zambiri zomvetsa chisoni zikuchitika padziko lonse, ena amadabwa ngati Yesuyo amatiganizira n’komwe. Inu mumaziona bwanji zimenezi?” Yembekezani ayankhe. Tsegulani pa mutu 24, ndi kukambirana mwachidule chifukwa chimene Yesu anabwerera padziko lapansi. Ndiyeno werengani Yohane 15:13, kugogomezera chikondi chochokera pansi pa mtima chimene Yesu ali nacho kwa ena.
“Munthu akangotchula Yesu Kristu, ambiri amaganiza za iye monga kamwana kapena munthu amene akuvutika atatsala pang’ono kufa. Zimene iwo amadziwa za Yesu ndizo kubadwa ndi kufa kwake basi. Zinthu zonse zabwino zimene ananena ndi kuchita pa moyo wake anthu saziganizira. Koma zimene anachita zimakhudza aliyense amene wakhala ndi moyo padziko lapansi lino. N’chifukwa chake tifunika kuti tiphunzire zonse zimene tingathe zokhudza zinthu zabwino zimene anatichitira.” Werengani Yohane 17:3. Tsegulani tsamba lokhala ndi mawu oyamba ndipo werengani ndime 4.
Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
“Kodi mukuganiza kuti dziko likanakhala labwinopo ngati anthu akanakhala kuti amatsatira mawu awa? [Werengani Mateyu 7:12a. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Buku ili lili ndi zinthu zambiri zimene tingaphunzire kwa mphunzitsi waluso woposa onse amene anakhalako.” Sonyezani zithunzi ndi mawu ofotokoza zithunzizo pa mutu 17.
“Makolo ambiri masiku ano amayesetsa kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zofunika? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Miyambo 22:6.] Onani kuti makolo akulimbikitsidwa kuyamba kuphunzitsa ana awo ali aang’ono. Buku ili lakonzedwa kuti liwathandize kuchita zimenezo.” Sonyezani zithunzi ndi mawu ofotokoza zithunzizo pa mutu 15 kapena 18.
“Nthawi zambiri makolo amadabwa ndi mafunso amene ana awo amafunsa. Ena mwa mafunsowo amakhala ovuta kuyankha, si choncho kodi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Aefeso 6:4.] Buku ili likhoza kuthandiza makolo kuyankha mafunso a ana awo masiku ano.” Sonyezani zithunzi zingapo ndi mawu ofotokoza zithunzi pa mutu 11 ndi 12 kapena 34 mpaka 36.
Yandikirani kwa Yehova
“Anthu ambiri amene amakhulupirira Mulungu amafuna kuti ayandikane naye kwambiri. Kodi mukudziwa kuti Mulungu amatipempha kuti tiyandikire kwa iye? [Werengani Yakobo 4:8.] Buku ili lakonzedwa kuti lithandize anthu kuyandikira kwa Mulungu pogwiritsa ntchito Baibulo lawo.” Werengani ndime yoyamba patsamba 16.
“Masiku ano dzikoli ladzala ndi kupanda chilungamo. Zinthu zikungofanana ndi mmene azifotokozera apa. [Werengani Mlaliki 8:9b.] Ambiri amakayika ngati Mulungu zimamukhudza n’komwe. [Werengani ziganizo ziwiri zoyambirira za m’ndime 4 patsamba 119.] Mutu umenewu ukufotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti kupanda chilungamo kukhalepo kwakanthawi.”