Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/06 tsamba 6
  • (1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) Mutu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • (1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) Mutu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 1/06 tsamba 6

(1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) Mutu

Njira yachidule yogawira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndiyo (1) kufunsa funso loti munthu anenepo maganizo ake, (2) kuwerenga lemba loyenerera, ndi (3) kumusonyeza mutu winawake m’bukuli umene ukulongosola nkhani mukukambiranayo pomuwerengera mafunso omwe ali koyambirira pansi pa mutuwo. Ngati mwininyumbayo ali ndi chidwi, mungagwiritse ntchito ndime zoyambirira za mutu umenewo pomusonyeza chitsanzo cha mmene timachitira phunziro la Baibulo. Njira imeneyi tingathe kuigwiritsa ntchito poyambitsa maphunziro pa ulendo woyamba kapena wobwereza.

◼ “Kodi mukuganiza kuti anthu a thupi lanyama ngati ifeyo tingathe kum’dziwa Mlengi, yemwe ali Wamphamvuyonse monga mmene lemba la m’Baibulo ili likunenera?” Werengani Machitidwe 17:26, 27, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 1.

◼ “Masiku ano pali mavuto ambiri, ndiye kodi mukuganiza kuti n’zotheka kupeza chitonthozo ndiponso chiyembekezo chimene chikunenedwa pa lemba ili?” Werengani Aroma 15:4, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 2.

◼ “Kodi mukanakhala ndi mphamvu zotha kusintha zinthu mukanatha kusintha zinthu kuti zikhale monga mmene lemba ili likulongosolera?” Werengani Chivumbulutso 21:4, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 3.

◼ “Kodi mukuganiza kuti kutsogolo kuno ana athu adzakhala m’dziko losangalatsa langati limene analilongosola mu nyimbo yakale iyi?” Werengani Salmo 37:10, 11, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 3.

◼ “Kodi mukuganiza kuti nthawi inayake mawu awa adzakwaniritsidwa?” Werengani Yesaya 33:24, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 3.

◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo ngati anthu akufa amadziwa zimene anthu amoyo akuchita?” Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Mlaliki 9:5, ndipo asonyezeni mutu 6.

◼ “Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kuti tsiku lina tidzaonanso okondedwa athu amene anamwalira, monga mmene Yesu ananenera pa mavesi awa?” Kenaka werengani Yohane 5:28,29, ndipo asiyeni ayankhe. Ndiyeno asonyezeni mutu 7.

◼ “Kodi mukuganiza kuti pakufunika chiyani kuti kufuna kwa Mulungu kuchitike padziko pano monga kumwamba, mogwirizana ndi zimene pemphero lotchuka ili limanenera?” Werengani Mateyu 6:9, 10, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 8.

◼ “Kodi mukuganiza kuti tikukhala mu nthawi imene inalongosoledwa mu ulosi uwu?” Werengani 2 Timoteo 3:1-4, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 9.

◼ “Anthu ambiri samvetsa kuti n’chifukwa chiyani mavuto a anthufe akumka aipiraipira. Kodi munayamba mwaganizirapo kuti zimene lemba ili likunena n’zimene zikuchititsa mavutowa?” Werengani Chivumbulutso 12:9, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 10.

◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo funso ngati ili?” Werengani Yobu 21:7, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 11.

◼ “Kodi mukuganiza kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo awa kungathandize anthu kukhala osangalala m’banja mwawo?” Werengani Aefeso 5:33, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 14.

Mungachitire lipoti phunziro la Baibulo ngati mwaphunzira maulendo awiri kuchokera pamene munasonyeza wophunzirayo kachitidwe kake ndipo zikuoneka kuti phunzirolo lipitirira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena