Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/06 tsamba 4-5
  • Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Armagedo
  • Baibulo
  • Banja
  • Imfa/Kuuka kwa Akufa
  • Masoka/Kuvutika
  • Moyo Wosatha
  • Nkhondo/Mtendere
  • Pemphero
  • Pokhala
  • Yehova Mulungu
  • Yesu Kristu
  • Zipembedzo
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • (1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) Mutu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 1/06 tsamba 4-5

Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani

Mphatika ino ili ndi malangizo osiyanasiyana ofotokoza mmene mungagawire buku la Baibulo limaphunzitsa chiyani. Kuti malangizowa akhale othandizadi m’pofunika kumvetsetsa mfundo zake zofunikira n’kuzinena mogwirizana ndi mmene inuyo mumalankhulira nthawi zonse. Muzilankhula mogwirizana ndi anthu a m’gawo lanulo, ndipo dziwani bwino mfundo za m’bukuli zimene mungazigwiritse ntchito pokambirana ndi anthu. Mungathenso kugwiritsa ntchito njira zina zomwe zingathandize m’gawo lanulo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsamba 8.

Armagedo

◼ “Anthu ambiri akamva mawu akuti ‘Armagedo,’ amaganiza za nkhondo yopulula anthu kwadzaoneni. Kodi mungadabwe kumva kuti Armagedo ndi nkhondo yofunika kuiyembekezera mosangalala? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Chivumbulutso 16:14, 16.] Taonani mawu awa onena za mmene moyo udzakhalire, nkhondo ya Armagedo ikadzachitika.” Pitani pa tsamba 82 mpaka 84, ndipo werengani ndime 21.

Baibulo

◼ “Nthawi zambiri anthu amati Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti zingatheke bwanji kuti buku lolembedwa ndi anthu litchedwe Mawu a Mulungu? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 2 Petro 1:21 ndiponso ndime 5 pa tsamba 19 ndi 20.] Buku ili limayankha mafunsowa pogwiritsa ntchito Baibulo.” Asonyezeni mafunso amene ali pa tsamba 6.

◼ “Masiku ano, anthu akudziwa zinthu zambiri kuposa kale. Koma kodi mukuganiza kuti tingapeze kuti malangizo amene angatithandize kukhala ndi moyo wosangalala ndiponso wabwino? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 2 Timoteo 3:16, 17 ndi ndime 12 pa tsamba 23.] Buku ili likulongosola mmene tingakhalire ndi moyo wosangalatsa Mulungu ndiponso wotipindulitsa.” Aonetseni tchati ndiponso chithunzi chimene chili pa tsamba 122 ndi 123.

Banja

◼ “Tonsefe timafuna kukhala ndi mabanja osangalala. Kodi si choncho? [Asiyeni ayankhe.] Baibulo limatchulapo chinthu chinachake chimene aliyense m’banja angachite kuti banja likhale losangalatsa. Chinthu chake ndicho kutsanzira Mulungu posonyeza chikondi.” Werengani Aefeso 5:1, 2 ndiponso ndime 4 pa tsamba 135.

Imfa/Kuuka kwa Akufa

◼ “Anthu ambiri amadzifunsa kuti chimachitika n’chiyani kwenikweni tikafa. Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kudziwa zimenezi? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Mlaliki 9:5 ndiponso ndime 5 ndi 6 pa tsamba 58 ndi 59.] Buku ili limalongosolanso momwe anthu amene anamwalira adzapindulire m’tsogolo, lonjezo la Mulungu lomwe lili m’Baibulo loti adzaukitsa akufa likadzakwaniritsidwa.” Asonyezeni chithunzi chimene chili pa tsamba 75.

◼ “Munthu amene timamukonda akamwalira, mwachibadwa timafuna kudzamuonanso. Kodi si choncho? [Asiyeni ayankhe.] Anthu ambiri alimbikitsidwa ndi lonjezo la m’Baibulo lonena za kuuka kwa akufa. [Werengani Yohane 5:28, 29 ndiponso ndime 16 ndi 17 pa tsamba 71 ndi 72.] Mutu umenewu umayankhanso mafunso amenewa.” Asonyezeni mafunso amene ali koyambirira pa tsamba 66.

Masoka/Kuvutika

◼ “Pakaoneka masoka, anthu ambiri amakayikira zoti Mulungu amaganiziradi anthu ndiponso zoti iyeyo amaona anthu akamavutika. Kodi inuyo munayamba mwaganizirapo nkhani imeneyi? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 1 Petro 5:7 ndi ndime 11 pa tsamba 11.] Buku ili limafotokoza momwe Mulungu adzathetsere mavuto onse a anthu.” Asonyezeni mafunso omwe ali koyambirira pa tsamba 106.

Moyo Wosatha

◼ “Anthu ambiri amafuna kukhala ndi thanzi labwino ndiponso moyo wautali. Koma kodi zikanakhala zotheka, mukanakonda kukhala ndi moyo wosatha? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Chivumbulutso 21:3, 4 ndiponso ndime 17 pa tsamba 54.] Buku lino likulongosola mmene tingakhalire ndi moyo wosatha ndiponso mmene moyo udzakhalire lonjezo limenelo likadzakwaniritsidwa.”

Nkhondo/Mtendere

◼ “Anthu padziko lonse amafuna mtendere. Koma kodi inuyo mumaona kuti n’zotheka kuti padziko pano padzakhale mtendere? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Salmo 46:8, 9.] Buku ili limalongosola mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake ndi kubweretsa mtendere padziko lonse.” Asonyezeni chithunzi pa tsamba 35, ndipo werengani ndime 17 mpaka 21 pa tsamba 33 ndi 34.

Pemphero

◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti Mulungu amayankha bwanji mapemphero? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 1 Yohane 5:14, 15 ndiponso ndime 16 mpaka 18 pa tsamba 170 mpaka 172.] Mutu umenewu umalongosolanso chifukwa chimene tiyenera kupemphera kwa Mulungu ndiponso zimene tiyenera kuchita kuti iye azimva mapemphero athu.”

Pokhala

◼ “M’madera ambiri, zikuvuta kwambiri kupeza malo abwino okhala omwe ali otsika mtengo. Kodi mukuganiza kuti nthawi inayake aliyense adzakhala ndi malo abwino okhala? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Yesaya 65:21,22 ndiponso ndime 20 pa tsamba 34.] Buku ili likulongosola mmene Mulungu adzakwaniritsire lonjezo lakeli.”

Yehova Mulungu

◼ “Anthu ambiri amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu amalakalaka atayandikana naye kwambiri. Kodi mukudziwa kuti Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyandikire kwa Mulungu? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Yakobo 4:8a ndiponso ndime 20 tsamba 16.] Buku ili analilemba n’cholinga choti lithandize anthu kudziwa zambiri zokhudza Mulungu, pogwiritsa ntchito Mabaibulo amene anthuwo ali nawo.” Asonyezeni mafunso omwe ali koyambirira pa tsamba 8.

◼ “Anthu ambiri amapemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti dzina la Mulungu ndani? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Salmo 83:18 ndiponso ndime 2 ndi 3 pa tsamba 195.] Buku limeneli limalongosola zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni zokhudza Yehova Mulungu ndi cholinga chake polenga anthu.”

Yesu Kristu

◼ “Anthu padziko lonse anamvapo za Yesu Kristu. Ena amanena kuti anali chabe munthu wotchuka basi. Ndiyeno pali ena amene amamulambira ngati Mulungu Wamphamvuyonse. Kodi inuyo mumaona kuti zimene munthu amakhulupirira pankhani ya Yesu Kristu zili ndi ntchito?” Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Yohane 17:3 ndiponso ndime 3 pa tsamba 37 ndi 38. Asonyezeni mafunso omwe ali koyambirira pansi pa mutu umenewo.

Zipembedzo

◼ “Anthu ambiri ayamba kuona kuti m’malo mothetsa mavuto ambiri amene tili nawowa, zipembedzo padziko lonse ndizo kwenikweni zikuyambitsa mavutowa. Kodi inuyo mukuganiza kuti zipembedzo zikutitsogolera ku njira yabwino? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Mateyu 7:13, 14 ndiponso ndime 5 pa tsamba 145 ndi 146.] Mutu uwu ukulongosola mfundo zisanu ndi chimodzi zodziwira kupembedza kumene Mulungu amavomereza.” Asonyezeni mfundo zimene azindandalitsa pa tsamba 147.

[Bokosi patsamba 5]

Njira Zouzira Anthu Kupereka Ndalama Mwakufuna Kwawo

“Ngati mutafuna kupereka kangachepe pofuna kuthandiza nawo pa ntchito yathu ya padziko lonse, zingakhale bwino kwambiri.”

“Mabuku athu sitigulitsa, koma timalandira kangachepe kalikonse kamene munthu angapereke pofuna kuthandiza nawo pa ntchito yathu ya padziko lonse.”

“Mwina mumadabwa kuti ntchito yathuyi timaiyendetsa bwanji. Ntchito imeneyi imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka padziko lonse mwakufuna kwawo. Ngati mungathe kupereka kangachepe panopo, tingayamikire kwambiri.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena