Kufalitsa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha
1 Yehova “ndiye Amene aphunzitsa munthu nzeru.” (Sal. 94:10) Iye amatigwiritsira ntchito kufalitsa chidziŵitso chonena za iye kwa anthu osadziŵa njira yomtumikira nayo imene amavomereza. Buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha lili chiŵiya chabwino chothandizira anthu oona mtima kupeza chidziŵitso cholondola chonena za Mulungu kuchokera m’Mawu ake olembedwa, Baibulo. (1 Tim. 2:3, 4) Kafotokozedwe komveka bwino ndi kotsatirika ka choonadi ka buku la Chidziŵitso kadzathandiza anthu kudziŵa zimene Yehova akufuna kuwaphunzitsa. Mwezi uno tikufuna kukambitsirana ndi anthu zimene zidzawachititsa kufuna kuŵerenga bukulo. Nawa malingaliro ena. M’malo moyesa kuloŵeza zimenezi, yesani kufotokoza mfundo zazikulu m’mawu anuanu ndi mwa kalankhulidwe kachibadwa.
2 Popeza kuti anthu ambiri anafedwapo wokondedwa wawo, mungaphatikize chiyembekezo cha chiukiriro m’kukambitsirana kwanu choyamba mwa kunena kanthu kena monga aka:
◼ “Ambiri tinafedwa wokondedwa wathu. Kodi munayamba mwaganizapo zakuti kaya mudzawaonanso? [Yembekezerani yankho.] Imfa siinalipo pachifuno choyambirira cha Mulungu popanga munthu. Yesu anapereka umboni wakuti okondedwa athu angaukitsidwe ku imfa. [Ŵerengani Yohane 11:11, 25, 44.] Ngakhale kuti zimenezi zinachitika zaka mazana ambiri kalelo, zimasonyeza zimene Mulungu walonjeza kutichitira. [ Tsegulani buku la Chidziŵitso pa chithunzi cha patsamba 85 ndi kuŵerenga mawu achithunzicho. Ndiyeno sonyezani chithunzi patsamba 86 ndi kukambapo.] Ngati mufuna kuŵerenga zambiri ponena za chiyembekezo chotonthoza chimenechi cha chiukiriro, ndingakonde kukusiyirani bukuli.” Ndiyeno ligaŵireni pachopereka cha nthaŵi zonse.
3 Pambuyo pa kukambitsirana koyamba pa za chiukiriro, mungayambe kukambitsirana kwanu kotsatira ndi munthu mmodzimodziyo motere:
◼ “Ndikhulupirira mukukumbukira zimene ndinanena tsiku lija kuti imfa siinali pa chifuno choyambirira cha Mulungu popanga munthu. Ngati zimenezo nzoona, nanga nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa? Akamba ena amakhala ndi moyo zaka zoposa 100, ndipo pali mitengo ina imene yakhalapo zaka zikwi zambiri. Nchifukwa ninji anthu amangokhala zaka 70 kapena 80? [ Yembekezerani yankho.] Timafa chifukwa chakuti anthu oyamba aŵiri sanamvere Mulungu.” Ŵerengani Aroma 5:12. Tsegulani patsamba 53 m’buku la Chidziŵitso ndi kuŵerenga mutu wake. Kambitsiranani ndime zoyambirira zitatu m’buku la Chidziŵitso, mukumasonyeza mayankho a mafunso olembedwawo. Lonjezani kudzabweranso kudzamaliza mutuwo. Limbikitsani munthuyo kumaliza kuuŵerenga wonse choyamba.
4 Ngati mulankhula kwa munthu wooneka kukhala wachipembedzo, munganene kuti:
◼ “Lerolino pali zipembedzo zosiyanasiyana mazana ambiri. Zonse zimaphunzitsa zosiyana. Anthu ena amanena kuti zipembedzo zonse nzabwino ndipo zimene timakhulupirira zilibe kanthu. Kodi inu muganiza bwanji? [Yembekezerani yankho.] Yesu anaphunzitsa chipembedzo choona ndipo anasonyeza kuti mitundu ina yakulambira inali yosalandirika kwa Mulungu. [Ŵerengani Mateyu 7:21-23.] Ngati tikufuna kukondweretsa Mulungu, tiyenera kulambira iye mogwirizana ndi chifuniro chake.” Tsegulani buku la Chidziŵitso pa mutu 5, ŵerengani mutuwo, ndi kusonyeza timitu tamkati. Longosolani kuti chidziŵitso chimenechi chimathandiza munthu kudziŵa mmene angakondweretsere Mulungu. Gaŵirani bukulo.
5 Anthu amene ali osokonezeka chifukwa cha zipembedzo zambiri zimene zilipo angakonde kumva yankho la funso ili paulendo wanu wobwereza:
◼ “Popeza kuti pali zipembedzo zambiri lerolino, kodi tingadziŵe motani chimene chili choona? Kodi mungafunefune chiyani chochidziŵirapo? [Yembekezerani yankho.] Yesu anatiuza mmene tingadziŵire otsatira ake oona.” Ŵerengani Yohane 13:35. Kambitsiranani ndime 18 ndi 19 m’mutu 5 wa buku la Chidziŵitso. Tchulani kuti mwa kugwiritsira ntchito zitsogozo za Malemba zimenezi ndi kupatula zosayenera, munthu akhoza kudziŵa chipembedzo choona. Simbani mmene Mboni za Yehova zilili zodziŵika kuzungulira dziko lonse kaamba ka chikondi chawo chenicheni ndi makhalidwe awo abwino kwambiri. Fotokozani mmene phunziro la Baibulo, mwa kugwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso, lingasonyezere bwino lomwe mtundu wa kulambira umene Mulungu amavomereza.
6 Ngati mukumana ndi kholo, kafikidwe aka kangakhale kogwira mtima:
◼ “Masiku onse timamva za kupulupudza kwa achichepere opanda makhalidwe konse. Achikulire ena amaimba mlandu masukulu kuti samaphunzitsa ana kudziŵa makhalidwe abwino ndi oipa. Kodi muganiza ndani amene ayenera kuwaphunzitsa zimenezi? [Yembekezerani yankho.] Mvetserani zimene Baibulo limanena pa funso limeneli. [Ŵerengani Aefeso 6:4.] Izi zimasonyeza kuti kuphunzitsa makhalidwe abwino ndiko thayo la makolo.” Tsegulani buku la Chidziŵitso patsamba 145, ŵerengani ndime 16, ndi kukambapo pa zithunzi za patsamba 147. Fotokozani kuti bukulo linakonzedwa kuti banja lonse liphunzirire pamodzi. Mwa kugwiritsira ntchito ndime 17 ndi 18 patsamba 146, sonyezani mmene timachitira phunzirolo ndi mabanja.
7 Ngati munayamba phunziro ndi kholo lodera nkhaŵa paulendo woyamba, mungalipitirize paulendo wobwereza mwa kunena kuti:
◼ “Dziko lamakono limapereka ziyeso zambiri kwa ana athu. Nchifukwa chake kumakhala kovuta kuti iwo awope Mulungu pamene akukula. Mwinamwake mukukumbukira kuti pamene tinakambitsirana tsiku lija, tinatchula mfundo ziŵiri. Monga makolo aumulungu, tiyenera kupereka chitsanzo chabwino kwa ana athu, ndipo tiyenera nthaŵi zonse kuwasonyeza chikondi chathu. Koma palinso chinthu china chimene Baibulo limanena kuti ana ayenera kuchilandira kwa makolo awo.” Ŵerengani Miyambo 1:8. Tsegulani patsamba 148 m’buku la Chidziŵitso ndi kupitiriza ndi phunzirolo, mukumakambitsirana ndime 19-23. Pemphani kuti mudzabwerenso kudzaphunzira ndi banja lonse, kuyambira pa mutu 1.