“Chikhulupiriro Chidza ndi Mbiri”
1 Titapeza wina ‘wofuna moyo wosatha,’ tifunikira kulimbitsa chikhulupiriro cha munthuyo mwa zinthu zimene wamva. (Mac. 13:48, NW; Aroma 10:17) Kuti tichite zimenezo, tiyenera kutsatira amene tinagaŵira magazini mwa kubwererako kuwaperekera makope atsopano ndi kukambitsirana nawo zochuluka. Tingagaŵirenso masabusikripishoni. Komabe, kumbukirani cholinga cha kuyambitsa phunziro m’buku lakuti Knowledge That Leads to Everlasting Life. Nazi njira zina zimene zingakhale zothandiza:
2 Paulendo wobwereza kwa amene munakambitsirana naye nkhani yakuti “Tamandani Mfumu Yamuyaya!,” mungayambe mwanjira iyi:
◼ “Pamene tinakambitsirana, tinapenda wina wa maumboni amphamvu osonyeza kuti Mulungu wamphamvuyonse aliko. Komabe, kungodziŵa kuti iye aliko sikokwanira. Tifunikira kudziŵa dzina lake. Kodi inu mumatcha Mulungu ndi dzina lotani? [Yembekezerani yankho.] Anthu ambirimbiri amamutcha kuti ‘Ambuye’ kapena ‘Mulungu,’ amene ali maina aulemu chabe. Ndiponso, iye amafuna kuti timdziŵe ndi dzina lake. [Ŵerengani Salmo 83:18.] Baibulo limatiuza zambiri ponena za Yehova Mulungu, monga momwe likufotokozera bukuli.” Sonyezani chithunzithunzi patsamba 29 la buku la Knowledge, ndipo ŵerengani mawu ake. Mutakambitsirana ndime zitatu zoyambirira m’mutu 3, mudzakhala mutayambitsa phunziro!
3 Kwa aja amene munakambitsirana nawo nkhani yakuti “Chifukwa Chake Chipembedzo cha Dziko Chidzatha,” mungafune kuwonjezera chidwi mwa kunena kuti:
◼ “Pambuyo poŵerenga nkhaniyi, mungakhale mutachita chidwi ndi choonadi chakuti sitingaone zipembedzo zonse mwa njira imodzimodzi. Zonse ziŵiri chipembedzo choona ndi chonyenga zilipo. Zimenezi zikubutsa funso loyenera lakuti, Kodi Mulungu amavomereza kulambira kwa yani? Yankho lake linaperekedwa ndi Yesu, ndipo lasonyezedwa m’bukuli.” Tsegulani pamutu 5 m’buku la Knowledge ndi kuŵerenga ndime 4, kuphatikizapo Yohane 4:23, 24. Ndiyeno funsani kuti, “Kodi mukufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere?” Ngati avomera, tsegulani pamutu 1 ndi kuyamba phunzirolo.
4 Ngati anachita chidwi ndi “Galamukani!” wa May 8, mutabwererako mungayese kafikidwe kotsatiraka kuyambitsa phunziro m’buku la “Knowledge”:
◼ “Ndikhulupirira mukukumbukira kuti tinakambitsirana za ziyembekezo zathu za kuona dziko lopanda nkhondo potsirizira pake. Nzovuta kuganizira mmene lidzakhalira. Nachi chithunzithunzi chake cholembedwa. [Sonyezani chithunzithunzicho pamasamba 188-9 m’buku la Knowledge.] Kodi sikudzakhala kosangalatsa kukhala m’malo otere? [Tsegulani pamasamba 4-5, sonyezani chithunzithunzi, ndipo ŵerengani bokosilo.] Mutu wa bukuli uli wofanana ndi mawu a Yesu opezeka pa Yohane 17:3. [Ŵerengani.] Ngati mungandilole, ndikufuna kukusonyezani mmene mungagwiritsirire ntchito bukuli ndi Baibulo lanu kupeza chidziŵitso chopulumutsa moyo.” Ngati mwini nyumba akufuna, yambani phunziro m’mutu woyamba.
5 Ngati munaonana ndi munthu amene anali wotanganitsidwa pamene munamfikira nthaŵi yoyamba, munganene zotsatirazi mutabwererako:
◼ “Ndinakuchezerani posachedwapa ndi kukusiyirani makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Magazini ameneŵa amakulitsa ulemu kaamba ka Baibulo ndi chitsogozo chake cha makhalidwe. Popeza ndiganiza kuti aliyense afunikira kumvetsa Mawu a Mulungu, ndabweranso kudzakusonyezani kanthu kena kamene kudzakuthandizani kuchita zimenezo.” Sonyezani buku la Knowledge, ndiponso sonyezani zamkati mwake patsamba 3. Mfunseni mutu umene wachita nawo chidwi, pitani ku umenewo, ndipo yambani phunziro.
6 Chimwemwe chathu chidzakula ngati titha ‘kutsegulira ena pakhomo la chikhulupiriro’ lotsogolera ku moyo wosatha.—Mac. 14:27; Yoh. 17:3.