Baibulo—Magwero a Chitonthozo ndi Chiyembekezo m’Dziko la Mavuto
1 Dzikoli laika mtundu wa anthu mu mkhalidwe wovuta kwambiri ndi wofunikira chitonthozo ndi chiyembekezo. Baibulo ndilo magwero okha a chitonthozo chenicheni. Limapatsa chiyembekezo cha dziko latsopano la chilungamo. (Aroma 15:4; 2 Pet. 3:13) Buku la Insight, Voliyumu 1, tsamba 311, limanena kuti: “Popanda Baibulo sitikanamdziŵa Yehova, sitikanadziŵa za mapindu abwino koposa a nsembe ya dipo ya Kristu, ndiponso sitikanazindikira zofunika zimene tiyenera kukwaniritsa kuti tikapeze moyo wosatha mu Ufumu wolungama wa Mulungu.”
2 M’November tidzapereka chisamaliro chapadera pa mbali imene Mawu a Mulungu, Baibulo, amachita pa kuthandiza anthu kulimbana ndi zovuta za dzikoli. Tidzagaŵira New World Translation of the Holy Scriptures ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Kodi tinganene chiyani chimene chidzathandiza anthu a maganizo abwino kuzindikira phindu la Baibulo?
3 Mutadzidziŵikitsa, munganene zonga izi:
◼ “Ndiyesa mukuvomereza kuti tazingidwa ndi mavuto omwe amatisoŵetsa mtendere wa maganizo. Kodi tingapeze kuti uphungu wothandiza umene ungatisonyeze mmene tingachitire ndi mavuto ameneŵa? [Yembekezani yankho.] Ine ndaona kuti Baibulo nlolimbikitsa kaamba kakuti limatiphunzitsa mmene tingakhalire achimwemwe. [Ŵerengani Luka 11:28.] Chifuno cha ntchito yathu ndicho kulimbikitsa anthu kuti aŵerenge Baibulo ndi kupindula ndi chilangizo chake. Buku ili lothandiza kuphunzira Baibulo lakuti, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lingakuthandizeni kuchita zimenezo. Onani zimene limanena kukhala chochititsa mavuto ochuluka a dzikoli. [Ŵerengani sentensi yachiŵiri ya ndime 9 patsamba 187.] Ngati mungakonde kuŵerenga bukuli, ndingakondwere kukusiyirani kope ili.” Tchulani chopereka cha panthaŵiyo.
4 Mwina mungasankhe kugwiritsira ntchito mafikidwe osavuta onga aŵa:
◼ “Timafuna kulimbikitsa ulemu wokulirapo pa Mawu a Mulungu, Baibulo. Ndikufuna kukupatsani trakiti limeneli lakuti, Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo. Limafotokoza chifukwa chake tiyenera kupita ku Baibulo kuti tipeze chiyembekezo chotsimikizirika cha dziko labwino kwambiri. [Tsegulani patsamba 6, ndi kuŵerenga Salmo 37:29 limodzi ndi ndime yothera.] Mudziŵerengere nokha trakitili, ndipo ndikadzabweranso ulendo wotsatira, ndidzafuna kudziŵa zimene mukuganiza ponena za chiyembekezo chimene Baibulo limapereka.”
5 Ofalitsa ena angafune kugwiritsira ntchito kafikidwe kolunjika koyambitsa phunziro la Baibulo kotere:
◼ “Ndafika kudzakupemphani kumaphunzira nanu Baibulo panyumba kwaulere. Baibulo linauziridwa ndi Mulungu, ndipo uphungu wake ungatithandize kuwongolera zinthu. New World Translation of the Holy Scriptures ya chilankhulo chamakono inalinganizidwira phunziro laumwini. Iyo yakondedwa kwambiri ndi oŵerenga Baibulo okwanira mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse. Lekani ndikusonyezeni mwachidule mmene mungaigwiritsirire ntchito. [Tsegulani patsamba 1653, ndipo msonyezeni pa 23A. Malinga ndi chikondwerero chosonyezedwa, ŵerengani lemba limodzi kapena aŵiri osonyezedwa ndi kukambitsirana mfundo imene ikuperekedwa. Fotokozani mmene kuŵerenga malemba osonyezedwa kudzasonyezera zimene Mulungu akufuna kuchita mwa Ufumu wake.] Ndidzakondwera kubweranso kuti tidzakambitsirane zowonjezereka pa chiyembekezo cha Ufumu umenewu.”
6 Baibulo ndilo magwero a chitonthozo ndi chiyembekezo limodzinso ndi choonadi chimene chingatitsogolere ku moyo wosatha. (Yoh. 17:3, 17) Kukambitsirana chidziŵitso cha Baibulo ndi ena kumakondweretsa Yehova, “amene afuna anthu onse apulumuke.”—1 Tim. 2:4.