Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/12 tsamba 1
  • Muzisamala Mukakhala mu Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzisamala Mukakhala mu Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 5/12 tsamba 1

Muzisamala Mukakhala mu Utumiki

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala tikakhala mu utumiki?

1 Atumiki a Mulungu amakhala ngati “nkhosa pakati pa mimbulu” pamene akulalikira ‘pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhotawu.’ (Mat. 10:16; Afil. 2:15) Anthu oipa ‘akuipiraipirabe.’ (2 Tim. 3:13) Umboni wa zimenezi ndi wakuti masiku ano anthu sakuchedwa kuyambitsa chisokonezo, kuchita zachiwawa ndiponso kuba anzawo powagwira mwankhanza. Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zingatithandize kuti ‘tizikhala ochenjera’ mu utumiki?—Mat. 10:16.

2. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingatichititse kuchoka m’gawo limene tikulalikira n’kupita kugawo lina?

2 Muzikhala Ochenjera: Lemba la Miyambo 22:3 limatiuza kuti ‘tizibisala’ tikaona tsoka. Choncho, muzikhala tcheru nthawi zonse. Zinthu zikhoza kusintha mwadzidzidzi m’gawo limene mumalalikiramo bwinobwino. Samalani mukaona apolisi akuyendayenda m’deralo kapena mukaona gulu la anthu mu msewu. Nthawi zina munthu wina wokoma mtima angakuchenjezeni. Zikatero, ndi bwino kuchoka m’deralo mwamsanga n’kupita kwina m’malo mofuna kuonetsetsa kuti chikuchitika n’chiyani.—Miy. 17:14; Yoh. 8:59; 1 Ates. 4:11.

3. Kodi mfundo ya pa Mlaliki 4:9 ingatithandize bwanji mu utumiki?

3 Musamayende Nokha: Lemba la Mlaliki 4:9 limati: “Awiri amaposa mmodzi.” Mwina munazolowera kuyenda nokhanokha mu utumiki popanda vuto lililonse. Koma kodi masiku ano ndi bwino kuyenda nokha? M’madera ena palibe vuto. Koma m’madera ena, si bwino kuti mlongo kapena wofalitsa wamng’ono azilalikira kunyumba ndi nyumba ali yekhayekha makamaka madzulo. Zimene zakhala zikuchitika zikusonyeza kuti ndi bwino kuyenda ndi mnzathu amenenso ali tcheru. (Mlal. 4:10, 12) Tikamalalikira tili kagulu, wofalitsa aliyense azionetsetsa zimene zikuchitikira anzake. Ngati mukufuna kuchoka m’gawolo mofulumirirapo, muziuza anzanu kuti mukuchoka.

4. Kodi tingatani kuti titeteze abale athu onse mumpingo?

4 Akulu ali ndi udindo wopereka malangizo malinga ndi mmene gawo lanu lilili, chifukwa ‘iwo amayang’anira miyoyo yathu.’ (Aheb. 13:17) Tikamatsatira malangizo awo ndiponso tikakhala odzichepetsa, Yehova adzatidalitsa. (Mika 6:8; 1 Akor. 10:12) Ife tonse atumiki a Mulungu, tiyeni tizilalikira mokwanira m’gawo lathu ndiponso tizikhala osamala nthawi zonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena