Nyimbo 58
Yehova, “Mulungu wa Chitonthozo Chonse”
1. Mulungu amatonthozadi;
Amatikonda zedi.
Titonthoze ena ndi Mawu,
Pansi pa Yesu Kristu.
2. Lero mavuto ngochuluka;
Tonse timawapeza.
Koma Yehova atonthoza,
Pokhala mboni zake.
3. Adalitsike Yehovayo;
Timalimbikitsidwa.
Adzatitsitsimula ndithu
Ngati tipilirabe.
4. Tonse tingapezedi mphamvu,
Poloŵa mumavuto.
Yesu anaphunzitsa kuti:
M’lungu amatikonda.