Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/95 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 1/95 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu January: Lililonse la mabuku amasamba 192 otsatirawa amene mipingo ingakhale nawo m’sitoko pa 40t limodzi: Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu; Commentary on the Letter of James; Is the Bible Really the Word of God?; Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?; Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo; Life Does Have a Purpose; Mbiri Yabwino—Yokusangalatsani ndi Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo! MUSAODE alionse a mabuku ameneŵa m’Chingelezi kapena m’Chibemba ku Sosaite pakuti kulibeko m’sitoko. Komabe, Sosaite ili ndi mtokoma waung’ono wa mabuku a Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo! m’Chicheŵa ndipo ameneŵa angaodedwe. Ngati mipingo ilibe alionse a mabuku ali pamwambawo m’sitoko, ingagaŵire buku la Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? February: Buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi lidzagwiritsiridwa ntchito. Mutagaŵira buku limeneli muyenera kupanga maulendo obwereza, ndipo muyenera kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. March: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. April ndi May: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.

◼ Mipingo iyenera kupanga makonzedwe oyenera akuchita Chikumbutso chaka chino pa Lachisanu, April 14, dzuŵa litaloŵa. Pamene kuli kwakuti ndi bwino kwa mpingo uliwonse kuchita Chikumbutso pa iwo wokha, nthaŵi zina zimenezi sizitheka. Kumene mipingo yochulukirapo imagwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu imodzi, mwina mpingo umodzi kapena ingapo ingagwiritsire ntchito malo ena madzulowo. Chikumbutso sichiyenera kuyamba mochedwa kwambiri kwakuti okondwerera chatsopano nkulephera kupeza nthaŵi yofikapo. Ndiponso, ndandanda yake siyenera kukhala yopanikiza kwambiri kwakuti nkulephera kupeza nthaŵi ya kupatsa moni alendo kuchiyambi ndi kumapeto kwa chochitikacho, kupanga makonzedwe akupereka chithandizo chauzimu chopitirizabe kwa ena, kapena ya kulimbikitsana kwa onse. Pambuyo popenda zonse zoloŵetsedwamo, akulu ayenera kupanga makonzedwe amene adzathandiza bwino lomwe awo opezeka pa Chikumbutso kupindula kwambiri ndi chochitikacho.

◼ Pa Sande, April 23, 1995, nkhani yapadera idzakambidwa m’mipingo yonse. Mutu wake udzakhala wakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira.” Tsimikizirani kuitanira onse amene adzapezeka pa Chikumbutso chaka chino. Kuyesayesa kwapadera kudzapangidwa kuthandiza ophunzira mamiliyoni ambiri amene akuchititsidwa maphunziro a Baibulo.

◼ Kuyambira mu February, ndipo mosapyola pa March 5, nkhani yapoyera yatsopano ya oyang’anira madera idzakhala yakuti “Chiphunzitso Chaumulungu Chilakika Padziko Lonse.” Imeneyi idzakhala nkhani yamasilaidi yosonyeza Misonkhano Yachigawo yapadera ya “Chiphunzitso Chaumulungu” yamitundu yonse imene inachitika m’zaka zautumiki za 1993 ndi 1994. Kumadera kumene masilaidi sadzakhalako kufikira panthaŵi ina pambuyo pake, oyang’anira madera adzakamba nkhani yakuti “Dalirani Mulungu wa Chitonthozo Chonse” ndi kupitirizabe kufikira pamene adzalandira masilaidi. Mipingo yonse itakhala ndi nkhani yamasilaidi, oyang’anira madera adzapitirizabe kukamba nkhani yakuti “Dalirani Mulungu wa Chitonthozo Chonse” kufikira pamene nkhani yatsopano ya woyang’anira dera idzakonzedwa kuchiyambiyambi cha 1996.

◼ Pa Msonkhano Wautumiki wa mlungu wa January 9, ofalitsa onse obatizidwa amene adzakhalapo adzapatsidwa makadi aumwini a Advance Medical Directive/Release ndi ma Identity Card a ana awo.

◼ Tikukumbutsanso mipingo yonse kuti ofalitsa ndi apainiya omwe sayenera kutenga magazini ndi mabuku pangongole. Onse ayenera kulipirira kashi zinthu zimenezi ndi masabusikripishoni aumwini olembetsedwa kupyolera mumpingo. Mwanjira imeneyi mudzakhalabe ndi maakaunti abwino ku Sosaite. Ngati muli ndi ngongole zilizonse zakale, muyenera kuyesetsa kuzisonkhanitsa mwa kukumbutsa mokoma mtima awo amene ali ndi ngongole kumpingo kuti alipire.

◼ Pakali pano Sosaite sikhoza kupereka makaseti ndi mavidiyo. Chonde musaode zilizonse za zinthu zimenezi kufikira mutaona chilengezo mu Utumiki Wathu Waufumu chonena za pamene mungaode zinthuzi ndi mmene mungaziodere.

◼ Chonde kumbukirani kuti ma mail transfer akubanki limodzi ndi S-20 siziyenera kutumizidwa mwachindunji ku nthambi ya Zambia ku Lusaka. Chonde zitumizeni ku keyala yotsatirayi: Watch Tower Society, P. O. Box 847, Blantyre, Malaŵi.

◼ Zofalitsidwa Zomwe Zilipo:

Chicheŵa: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. (laling’ono).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena