Kugwiritsira Ntchito Bwino Mabuku Athu Akale
1 Yehova watipatsa chakudya chauzimu chambiri. Chochuluka cha chakudya chimenechi chili m’mabuku amasamba 192 amene afalitsidwa m’zaka zaposachedwapa. M’January tidzakhala tikugaŵira buku lililonse lamasamba 192 malinga ndi chilengezo chonena za chogaŵira cha m’January. Kodi muli ndi ena a mabuku ameneŵa kunyumba amene akali mumkhalidwe wabwino? Kodi mpingo uli ndi ena m’sitoko? Ngati ndi choncho, kungakhale bwino kupenda zamkati mwake ndi kusankha mfundo zina zokambitsirana zimene mungagwiritsire ntchito mu ulaliki wanu.
2 Ngati mukugwiritsira ntchito buku la “Mbiri Yabwino—Yokusangalatsani,” mutauza mwininyumba dzina lanu mungonena kuti:
◼ “Ndafika pano kudzakupatsani uthenga wachiyembekezo umene udzakusangalatsani tsiku lalero. Ndikhulupirira kuti mukuvomereza kuti maboma aumunthu sangathetse mavuto a anthu. Imeneyo ndiyo mfundo imene Salmo la Baibulo likunena pa vesi 3 m’chaputala cha 146. [Ŵerengani.] Mankhwala achikalire a mavuto a anthu ndiwo boma la Ufumu wa Mulungu mwa Kristu basi. Umenewo ndiwo mutu waukulu wa Baibulo ndipo wafotokozedwa bwino lomwe m’bukuli limene ndifuna kukusiyirani pa 40t chabe.” Lonjezani kuti mudzabweranso kudzakambitsirana zowonjezereka.
3 Ngati mukugwiritsira ntchito buku la “Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?,” mungayese kafikidwe kotsatiraka:
◼ “Anthu ambiri amavutika ndi kufunafuna chimwemwe m’dzikoli chifukwa muli mavuto ambiri. Kodi muganiza kuti kuli kotheka kukhala achimwemwe ndi mikhalidwe imene ilipoyi? [Yembekezerani yankho. Tsegulani patsamba 5, ndime 2, ndi kusonyeza mavuto ena ofala amene amatidetsa nkhaŵa.] Baibulo limasonyeza mmene tingalimbanirane ndi mavuto ameneŵa ndi mmene potsirizira pake tingapezere chimwemwe chosatha m’dziko latsopano lamtendere. [Ŵerengani Yesaya 32:17, 18.] Baibulo limapereka uphungu wolunjika umene ungatithandize kupeza chimwemwe chokulirapo m’moyo. Buku limeneli lili ndi uphungu umenewu ndipo limafotokoza mmene tingaugwiritsirire ntchito.”
4 Ngati mukugwiritsira ntchito buku la “Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo,” mwina mungafune kuyesa zotsatirazi:
◼ “Anthu ambiri amene amafuna kuwongolera moyo wawo atembenukira ku chipembedzo. Koma ambiri mwa ameneŵa adakali osakondwa. Kodi mwaona zimenezo? Kodi muganiza kuti nchifukwa ninji zili choncho? [Yembekezerani yankho.] Ndaona mawu awa kukhala ondikondweretsa kwambiri. [Ŵerengani patsamba 8, ndime 8 mpaka pa Mateyu 7:23.] Zimenezi zimayika chitokoso chachikulu pa anthu oona mtima amene akufuna kudziŵa ophunzira a Kristu, sichoncho kodi? Taonani mbali iyi ya ndime 9. [Ŵerengani ziganizo zitatu zoyambirira.] Kodi zimenezi sizosangalatsa? Zimenezi nzimene Yesu analonjeza pa Marko 10:29, 30. [Ŵerengani.] Ubale wamitundu yonse wa panthaŵi imeneyo udzakhala padziko lonse. Bukuli, Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo, lidzakuthandizani kuphunzira zambiri ponena za malonjezo a Mulungu. Ndikulimbikitsani kutenga limodzi. Lingakhale lanu pa 40t.”
5 Mwina mungafune kugwiritsira ntchito brosha la “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” Ngati ndi choncho, mukhoza kunena zotsatirazi:
◼ “Anthu ambiri amafuna kudziŵa chifukwa chimene Mulungu amalolera anthu kuvutika kwambiri m’dziko. Popeza kuti iye ali wamphamvuyonse, bwanji sachitapo kanthu kuthetsa mavuto athu? Muganiza bwanji? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatitsimikiziritsa kuti Mulungu sanatitaye.” Tsegulani patsamba 27, ndime 22, ndi kuŵerenga Salmo 37:11, 29. Sonyezani chithunzi chokongola chosonyeza zimene tingayembekezere. Ngati broshalo lilandiridwa, pemphani kuti mudzabwerenso kudzasonyeza mmene lingagwiritsiridwire ntchito kuphunzira Baibulo.
6 Mabuku athu asonkhezera anthu zikwi zambiri kupenda Baibulo mosamalitsa. Zimene aphunzira zawapatsa chiyembekezo cha mtsogolo mwachimwemwe. (Sal. 146:5) Ndi mwaŵi wathu kuwathandiza.