Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/95 tsamba 8
  • Sonyezani Kuti Mumasamala mwa Kupanga Maulendo Obwereza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sonyezani Kuti Mumasamala mwa Kupanga Maulendo Obwereza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Pangani Maulendo Obwereza pa Mabrosha Onse Amene Munagaŵira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kugwiritsira Ntchito Bwino Mabuku Athu Akale
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 1/95 tsamba 8

Sonyezani Kuti Mumasamala mwa Kupanga Maulendo Obwereza

1 Kufunafuna anthu okondwerera kunyumba ndi nyumba kumasonyeza chikhumbo chanu cha kupatsa ena mwaŵi wa kumva uthenga wa Ufumu. Chotero tsimikizirani kubwerera kumene mwagaŵira mabuku m’mwezi uno wa January, pakuti imeneyi ndiyo njira yabwino yosonyezera kuti mumasamala anthu ena.

2 Ngati munagaŵira buku la “Mbiri Yabwino Yokusangalatsani” mungayese kupitiriza makambitsirano mwanjirayi:

◼ “Tsiku lija tinakambitsirana za Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzatichitira. Ufumu umenewo posachedwapa udzasanduliza dziko lapansili kukhala paradaiso. Popeza kuti sitinaonepo paradaiso, kungakhale kovuta kulingalira mmene adzakhalira. Komabe, paradaiso ameneyo walonjezedwa m’Baibulo. [Ŵerengani Salmo 72:7.] Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chikufunikira kwa ife kuti tidzakhale nzika za dziko latsopano lamtendere limenelo?” Lolani mwininyumbayo kukambapo, ndiyeno msonyezeni mfundo ili pa Salmo 37:9, 11, 29.

3 Nali lingaliro limene mungagwiritsire ntchito pobwerera kumene munagaŵira buku la “Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?”:

◼ “Tonsefe timafuna kukhala achimwemwe. Ambiri amaganiza kuti chimwemwe chenicheni nchosatheka m’dzikoli. Kodi inu muganiza bwanji? [Yembekezerani yankho.] Kwanenedwa kuti chimwemwe chili mkhalidwe wa maganizo. Ngati maganizo athu ali odzala ndi chikondi kwa ena, ulemu kwa Mulungu, ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo, tingakhale ndi chimwemwe chenicheni mosasamala kanthu za mavuto athu.” Ŵerengani Salmo 119:1, 2. Fotokozani kuti phunziro la Baibulo limatiphunzitsa mmene tingakondere ena, kusonyeza ulemu kwa Mulungu, ndi kupeza chiyembekezo chotonthoza cha mtsogolo.

4 Mungabwerere kumene munagaŵira buku la “Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo,” ndi ulaliki wachidule wonga wotsatirawu:

◼ “Tsiku lija pamene ndinabwera kuno, tinakambitsirana mmene aliyense angakondere kukhala m’dziko lamtendere ndi chisungiko. Kodi muganiza kuti nchifukwa ninji Mulungu wayembekezera kwa nthaŵi yaitali motere popanda kuchitapo kanthu kuwongolera mkhalidwe wa anthu? [Ŵerengani 2 Petro 3:13, ndipo sonyezani mwininyumba tsamba 186, ndime 22, m’bukulo.] Kodi si zoona kuti munthu angakulitse kuleza mtima mothandizidwa ndi Mawu a Mulungu? Ndifuna kukusonyezani mmene bukuli lingakuthandizireni.”

5 Mungabwerere kumene munagaŵira brosha la “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” mwa kugwiritsira ntchito lingaliro lotsatirali:

◼ “Tsiku lija ndinakusiyirani broshali, limene limafunsa funso lofunika kwambiri lakuti: ‘Kodi Mulungu amatisamaliradi?’ Pambuyo poŵerenga brosha ili, kodi munapeza chiyani? [Yembekezerani yankho.] Mwachionekere munalimbikitsidwa mwa kuŵerenga malemba amene amalonjeza za dziko latsopano laparadaiso, mmene tidzakhoza kukhala pamtendere. [Sonyezani zithunzi zimene zili pamasamba 2 ndi 3, ndipo sonyezani mbali zina zosangalatsa za dziko latsopano.] Ndikhulupirira inu ndi okondedwa anu mungakonde kukhala m’dziko lotere. Taonani zimene ndime 16 patsamba 31 ikunena pa zimenezi.” Ŵerengani ndimeyo, ndiyeno tchulani kuti kufunafuna Yehova kumatanthauza kuphunzira zambiri ponena za iye ndi zifuno zake mwa kuphunzira Mawu ake, Baibulo.

6 Yehova wapereka chitsanzo changwiro monga Mbusa wachikondi amene amasamalira nkhosa zake. (Ezek. 34:11-14) Kuyesayesa kwathu ndi mtima wonse kutsanzira chisamaliro chake chachikondi kumamkondweretsa, kumasonyeza chikondi chathu, ndipo kumadzetsa madalitso kwa ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena