Kulalikira—Mwaŵi Wolemekezeka
1 Utumiki wa mbiri yabwino uli mwaŵi wolemekezeka umene Yehova watipatsa. (Aroma 15:16; 1 Tim. 1:12) Kodi ndimo mmene mumauonera? Kupita kwanthaŵi kapena kuseka kwa ena sikuyenera kuloledwa kuti kuziralitse kufunika kwake m’kaonedwe kathu. Kunyamula dzina la Mulungu ndiko ulemu woperekedwa kwa oŵerengeka okha. Kodi ndimotani mmene tingakulitsire chiyamikiro chathu cha mwaŵi umenewu?
2 Kulalikira uthenga wa Ufumu sikumatichititsa kuyanjidwa ndi dziko. Ambiri amaona ntchito yathu mwamphwayi kapena monyalanyaza. Ena amaiseka kapena kuitsutsa. Chitsutso chotero chingachokere kwa ogwira nawo ntchito, anansi, kapena ngakhale ziŵalo za banja. M’maso mwawo tingaonekere kukhala osokeretsedwa ndi opusa. (Yoh. 15:19; 1 Akor. 1:18, 21; 2 Tim. 3:12) Mawu awo olefula maganizo ngolinganizidwa kufooketsa changu chathu ndi kutichititsa kubwerera m’mbuyo kapena kulekeratu mwaŵi wathu wolemekezeka. Malingaliro osakondweretsa amachirikizidwa ndi Satana, amene ‘wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero . . . chisawaŵalire.’ (2 Akor. 4:4) Kodi mumachita motani?
3 Nkofunika kukumbukira kuti kulalikira kwathu za Ufumu ndiko ntchito yofunika koposa imene aliyense wa ife ayenera kuchita lerolino. Tili ndi uthenga wopulumutsa moyo umene sumapezeka mwanjira ina iliyonse. (Aroma 10:13-15) Kukhala ndi chivomerezo cha Mulungu, osati cha munthu, ndi kumene kuli kofunika. Lingaliro la dziko losakondwera ndi ntchito yathu yolalikira silimatiletsa kulalikira mbiri yabwino molimbika.—Mac. 4:29.
4 Yesu anaŵerengera kwambiri mwaŵi wake wa kuchita chifuniro cha Atate wake. (Yoh. 4:34) Anadzipereka kotheratu pa utumiki ndipo sanalole zocheukitsa kapena otsutsa kummbweza m’mbuyo. Kulalikira uthenga wa Ufumu nthaŵi zonse kunali koyamba m’moyo wake. (Luka 4:43) Tikulamulidwa kutsanzira chitsanzo chake. (1 Pet. 2:21) Pochita zimenezo, timatumikira monga “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Kodi tikugwiritsira ntchito mokwanira mwaŵi umenewu? Kodi timafunafuna nyengo za kuuza ena mbiri yabwino molinganizidwa ndi mwamwaŵi? Monga Mboni za Yehova, nthaŵi zonse tiyenera kukhala okonzekera ‘kulengeza poyera dzina lake.’—Aheb. 13:15, NW.
5 Phande lathu mu utumiki kwakukulukulu limadalira pa mkhalidwe wathu wamaganizo. Kodi timayamikira kwambiri zonse zimene Yehova watichitira? Kodi takulitsa m’mitima mwathu kukonda Yehova kumene kumatisonkhezera kuchita zonse zimene tikhoza mu utumiki wake? Kusinkhasinkha pa madalitso amene tili nawo tsopano lino ndiponso pa zimene Yehova walonjeza kaamba ka mtsogolo kumatithandiza kukhala ndi chikondi chachikulu kwa Mlengi wathu. Chikondi chotero chimatisonkhezera kuchitapo kanthu—khama ndi kukhala wanthaŵi zonse mu ntchito yolalikira Ufumu kufikira ku mlingo umene mikhalidwe yathu imatilola. Changu chathu chidzapereka umboni wa kukonda kwathu Yehova ndi mnansi wathu.—Marko 12:30, 31.
6 Timasonyeza mmene timaŵerengerera kwambiri kanthu kena mwa zimene timachita ndi kunena za iko. Kodi timaŵerengeradi mwaŵi wathu wa kulalikira za Ufumu? Kodi timalemekeza utumiki wathu? Kodi tili otsimikiza mtima kuchita khama m’ntchito yofunika imeneyi mosasamala kanthu za chitsutso? Ngati timalemekeza kwambiri mwaŵi umenewu wabwino kwambiri, ndithudi tidzakhala achangu ndi amtima wonse.—2 Akor. 4:1, 7.