Kulalikira Ufumu—Ntchito Yofunika Zedi
1 Tsiku lililonse, Yehova moolowa manja amasamalira miyoyo miyandamiyanda ya anthu a padziko lapansi. (Mat. 5:45) Komabe, ndi anthu owerengeka chabe amene ali ndi mwayi wapadera wothokoza Mlengi wawo mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14) Kodi ntchito imeneyi mumaiona kukhala yofunika kwambiri?
2 Kulalikira Ufumu kumalemekeza Mulungu ndiponso kumapereka chiyembekezo ndi mtendere kwa anthu amene ali opsinjika nthawi zovuta zino. (Aheb. 13:15) Amene amalabadira uthengawu amakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kodi ndi ntchito yotani yomwe mungaphunzire kapena kuichita imene ingakupindulireni kwambiri choncho? Mmene mtumwi Paulo anachitira utumiki wake zikusonyeza kuti anali kulemekeza utumikiwo. Anauona monga chuma cha mtengo wapatali.—Mac. 20:20, 21, 24; 2 Akor. 4:1, 7.
3 Kuyamikira Ntchito Yathu Yofunika Zedi: Njira imodzi yomwe tingasonyezere kuti tikuyamikira ntchito yathu yolalikira ndiyo kuonetsetsa kuti tikuigwira bwino. Kodi timapeza nthawi yokonzekera ulaliki wathu kuti ukawafike pamtima omvera athu? Kodi tingasule luso lathu lofotokozera Malemba komanso lokambirana ndi anthu? Kodi timalalikira m’gawo lathu lonse mosamalitsa? Kodi timatha kuyambitsa ndi kuchititsa phunziro la Baibulo? Mofanana ndi Akristu okhulupirika, akale ndiponso amakono, ifenso timachita ntchito imeneyi chifukwa chozindikira kufunika kwake. Ndipo timanyadira mwayi wathu wa utumiki.—Mat. 25:14-23.
4 Pamene tikulimbana ndi mavuto obwera chifukwa cha ukalamba, matenda, kapenanso zinthu zina, n’zotonthoza kudziwa kuti khama limene timalisonyeza mu utumiki limayamikiridwa kwambiri. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova amayamikira tikamachita khama pomutumikira, ngakhale tikamachita zinthu zimene kwa anthu zingaoneke ngati zazing’ono.—Luka 21:1-4.
5 Kulalikira Ufumu kumabweretsa chimwemwe chachikulu. Mlongo wina wa zaka 92 anati: “Ndimaona kuti ndili ndi mwayi kwambiri ndikaganizira zaka zoposa 80 zimene ndatumikira Mulungu modzipereka, ndipo sindidandaula ayi! Zikanatheka kubwerera ku unyamata, ndikanasankha moyo womwewu, chifukwatu, ‘chifundo cha Mulungu chimaposa moyo makomedwe ake.’” (Sal. 63:3) Nafenso tiyamikire ntchito yapadera imene Mulungu watipatsa—ntchito yolalikira Ufumu.