Muziona Mwayi Wanu wa Utumiki Monga Chinthu Chamtengo Wapatali
1. Kodi anthu ambiri m’dzikoli amaona bwanji ntchito yathu yolalikira?
1 Anthu ambiri m’dziko la Satanali amaona ntchito yathu yolalikira ngati chinthu “chopusa.” (1 Akor. 1:18-21) Ngati sitisamala, maganizo olakwika amenewa akhoza kutifooketsa ndipo tingayambe kugwira ntchitoyi mosaikirapo mtima. (Miy. 24:10; Yes. 5:20) Koma kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuona mwayi wathu wokhala Mboni za Yehova monga chinthu chamtengo wapatali?—Yes. 43:10.
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolalikira ndi ‘ntchito yapatulika’?
2 ‘Ntchito Yopatulika’: Mtumwi Paulo anafotokoza kuti ntchito yolalikira ndi ‘ntchito yopatulika.’ (Aroma 15:15, 16) Kodi ntchito yolalikira ingakhale bwanji ‘ntchito yopatulika’? Tikamagwira nawo ntchitoyi timakhala “antchito anzake” a “Woyera” amene ndi Yehova ndipo timathandizira kuti dzina lake liyeretsedwe. (1 Akor. 3:9; 1 Pet. 1:15) Yehova amaona kuti tikamalalikira nawo timakhala tikupereka ‘nsembe zomutamanda’. Choncho, utumiki wathu ndi mbali yofunika kwambiri ya kulambira kwathu.—Aheb. 13:15.
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova watilemekeza potipatsa mwayi wogwira nawo ntchito yolalikira?
3 Ntchito yolalikira ndi ntchito yolemekezeka kwambiri imene inaperekedwa kwa anthu ochepa okha. Angelo akanasangalala kwambiri kugwira ntchito imeneyi ndipo mosakayikira akanatha kuigwira bwino kwambiri. (1 Pet. 1:12) Koma Yehova anasankha ifeyo anthu opanda ungwiro, ‘zonyamulira zoumbidwa ndi dothi,’ kuti tigwire ntchito yapamwamba imeneyi.—2 Akor. 4:7.
4. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona ntchito yolalikira kukhala yamtengo wapatali?
4 Ntchito Yofunika Kukhala Patsogolo pa Zonse: Chifukwa chakuti timaona kuti ndi mwayi kulalikira uthenga wabwino, ntchitoyi timaiona kukhala ‘yofunika kwambiri’ pamoyo wathu. (Afil. 1:10) Choncho, mlungu uliwonse timapatula nthawi kuti tizigwira nawo ntchito imeneyi. Munthu woimba amene amaona kuti ali ndi mwayi wamtengo wapatali pokhala m’gulu lotchuka padziko lonse, angafunike kukonzekera kuti akaimbe bwino nyimbo iliyonse komanso mwaluso kwambiri. Mofanana ndi woimbayu, ifenso tiyenera kukonzekera tisanapite kokalalikira kuti ‘tikaphunzitse ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ Komanso tidzayesetsa kukulitsa “luso la kuphunzitsa.”—2 Tim. 2:15; 4:2.
5. Kodi ndani amene amayamikira ntchito yathu yolalikira?
5 Musafooke anthu ambiri akamakana kumvetsera uthenga wathu. Dziwani kuti pali anthu ambiri m’gawo lathu amene amamvetsera. Ndipotu ifeyo sitikufuna kusangalatsa anthu. Amene tikufuna kumusangalatsa ndi Yehova ndipo amayamikira kwambiri khama lathu.—Yes. 52:7.